Chichewa

Msika wa fodya wa okushoni ukuponderezedwa

 

Kampani yoyendetsa malonda a fodya pamsika wa okoshoni ya AHL Group yauza alimi kuti akhale tcheru pogulitsa fodya wawo pa mgwirizano ati kaamba koti cholinga cha ogula fodyawa chokola alimi muukonde wa mgwirizano kuti mtsogolumu alimiwa adzakhale opanda liwu pafodya wawo.

Mkulu wa zamalonda kukampaniyi Moses Yakobe adauza alimi a fodya ku Lufita, m’boma la Chitipa Lachiwiri kuti cholinga cha kampani zogula fodya nkuthetsa msika wa okushoni poika alimi onse pa mgwirizano.

Msika wa fodya wa okushoni
Msika wa fodya wa okushoni

“Tikasiyanitsa Malawi ndi maiko oyandikana nawo monga Mozambique komwe kulibe okushoni, alimi kumeneko akuvutika chifukwa ogula fodya ndi womwe ali ndi ulamuliro onse; osati olima fodya,” Yakobe adatero.

Iye adati izi zaonekera pamsika wa fodya wa bale chaka chino pomwe alimi omwe adatenga ngongole kukampani zogula adagulidwa pamtengo wabwino wa $1.79 (pafupifupi K700).

Yakobe adati alimi omwe adali pa mgwirizano koma sadatenge ngongole adagulitsa pamtengo wa $1.64 ndipo zidavutiratu pa okushoni pomwe fodya adagulidwa pa mtengo wotsikitsitsa wa $1.46.

“Polongosola ogulawo adati alimi omwe adatenga ngongole adagulidwa fodya wawo pamtengo wokwererapo kuti apereke ngongole msanga.

“Apa chidakula ndikukondera popeza alimi enawanso adakatenga ngongole paokha ena adafufuza ndalama paokha. Koma pano akugulitsa fodya wawo pamtengo wotsika zedi chifukwa choti sadatenge ngongole ku kampani zogula fodya,” Yakobe adatero.

Izi zili chonchi, mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira-Banda wapempha boma kuti lithetse chilinganizochi chimene chidayamba mu 2012.

“Tangoganizani, chaka chino alimi ena amene anali pakontilakiti adagulitsa fodya wawo pa okushoni. Tikufuna alimi athu azipindula, zimene sizingatheke ngati ogula akhala ndi mphamvu zolenga mitengo,” adatero iye. n

 

 

 

 

Related Articles

Back to top button