Chichewa

Msika wa ziwala, mbewa

Listen to this article

 

Tidali pamalo aja timakonda pa Wenela, mnyamata uja Bonny Wasawaliya Kanindo atafika ku nyumba ya ulemu ku Nyumba ya Malamulo komwe adakakwanitsa kupereka chikalata chodzudzula zophana.

“Ndinakaperekera chikalatacho m’chimbudzi chifukwa ndimafuna ndikapereke ndili chinochino. Zatheka,” adatero Kanindo.

“Koma ayi ndithu mwaitha, uthenga wamveka ndipo tikudziwa amene amakonza zionetsero n’kumayenda okhaokha atangerapo phunziro,” adatero Abiti Patuma.

Kanindo adati tisachedwe pamalopo, koma titsagane naye kupita ku Limbuli komwe amafuna akakhale limodzi ndi Moya Pete amene amati akakambe za chimanga chimene chimapezeka kwambiri.

“Mwayi wathu ndi womwewu, tikaguleko chimanga chifukwa pa Wenela chimanga ndiye chadula. Mwati pofika December sichikwana K25 000?”

art

Chongofika pa Limbuli, tidapeza atate, akazi awo ndi ana awo akudikira Moya Pete yemwe nthawiyo akumwa tiyi pamwala uja ankawerengera Chilembwe ku PIM m’boma la Chiradzulo.

Anthu adamupatsa molalo Kanindo. Koma tidaona akuluakulu ena akulozerana zala.

Atafika Moya Pete, kudaterera. Ndidamuona akunong’oneza mmodzi mwa asirikali ake. Kenako adamuloza Kanindo.

Ndidangoona asirikali aja akukhamukira kwa Kanindo, kodi kapena dzina lake ndi Kawindo?

“Iwe uchoke pano. Moya Pete akuti akufuna achite zisudzo aseketse anthu chikhakhali. Zisudzo unachita iwe zabunobuno zija akuti wachepa nazo,” adamuuza.

Padalibe zaulemu, adamukoka kumutengera kugalimoto yake yolemba Wikoni 1.

Moya Pete adaimirira. Kumanja kwawo kudali nsalu ya mtundu wa thambo.

“Inu! Inu! Mumadziwa za dirama kwambiri inu? Inetu ndidali wadirama kalelo. Zisudzo si nkhani. Mr Bean, Trevor Noah, Anne Kansiime mukutamayu, Teacher Mpami what? Onsewo ndaphunzitsa ndekha,” adayamba motero.

Anthu onse adafa nalo phwete! Sindikudziwa ngati amaseka zimene amanena Moya Pete kapena amawaseka!

“Ndikuuzeni kwambiri! Tiyeni tizidya utakafumbi! Tiyeni zithuli zagundikazi tisazilekerere. Tasekani kwambiri,” adatero.

Anthu adaseka. Ha! Ha! Ha! Abiti Patuma amvekere: “Ki! Ki! Ki! Lol!”

Moya Pete adamezera malovu.

“Inutu mukudziwa kwambiri. Chimanga chikupezeka kwambiri kuno ku Limbuli kokha kuno. Choncho, tiyeni tizingotafuna akapuko….amkokamadzi. Mukapezanso makoswe mukhoza kuchita nawo, samapha konse. Sekani kwambiri anthu inu!” adapitiriza.

Anthu adaseka chikhakhali. Sindinaone munthu wodziwa kuseketsa ngati Moya Pete!

“Choncho! Ndachotsa chimanga chija adaika mkulu uja Mfumu Mose chifukwa pano chikusowa. Mbewa ndi zithuli ndizo tiziike apa! Muzidya zimenezi. Mwamva kwambiri?” adafunsa.

Pomwe amatero nkuti akutambasula nsalu yatsopano ija.

Ndikumbuka bwino lomwe gogo uja adandipeza ndikulima osavala ankakonda kunena kuti safuna anthu ake azigona m’nyumba zothonya mvula ikamagwa, azidya ndi kuvala bwino; ndidakumbukanso Mpando Wamkulu akunena kuti mukamva njala kaya minkhaka zitafunani….

“Kodi tsono enatu sadya mbewa ndiye azidyanji?” ndidafunsa.

Moya Pete adangotsonya!

Gwira bango iwe, upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button
Translate »