Chichewa

Msika wa zondeni ngosayamba

Listen to this article

 

Katswiri wa zamadyedwe m’dziko muno, Chrispine Jedegwa, akupanga ndi kugulitsa ufa wa mbatata ya kholowa yamakolo yotchedwa zondeni yomwe akuti ili ndi ufa wapamwamba wopatsa thanzi.

Anthu ambiri adazolowera kuti ufa umapangidwa kuchokera kuchimanga ndi chinangwa basi koma katswiriyu wati phindu lochokera m’mbatata limachuluka mbatatayo ikagayidwa n’kugulitsa ufa wake.

“Alimi ambiri sakonda kulima mbatata ya zondeni chifukwa sibereka kwambiri koma chomwe sadziwa n’chakuti mbatatayi ili ndi mphamvu ya mankhwala ndipo muli ndalama zochuluka,” adatero Jedegwa.

Jedegwa: Ufa wa zondeni tikaukonza umakhala ngati uwu
Jedegwa: Ufa wa zondeni tikaukonza umakhala ngati uwu

Iye adati mbatatayi ikacha ndipo mukaimuka bwinobwino mukaigaya mukhoza kupanga ufa wophikira phala kapena chakudya china chilichonse ndipo munthu akadya phalalo thupi lake limakulupala.

Mkuluyu adati alimi alime mbatata ya mtunduwu kwambiri powatsimikizira kuti msika wake ulipo wosayamba.

“Pakalipano mbatatayi ikulimidwa kwambiri ndi alimi a ku Thyolo, Phalombe, Kasungu ndi Mchnji koma sakukwanitsa pomwe ife timafuna moti alimi omwe akufuna kupha makwacha alime mbatata yamtunduwu ndipo tikulonjeza kuti tidzawagula,” adatero Jedegwa.

Iye adatinso alimi atafuna mbewu ya mbatatayi yobereka kwambiri akhoza kukumana ndi akuluakulu a kampani ya C & NF omwe akupanga ufawu chifukwa mbewuyi alinayo yambiri.

Alimi ambiri amadandaula kuti amalephera kulima mbewu zina polingalira nkhani ya msika koma Jedegwa watsimikiza kuti kampani yawo njokonzeka kugula mbatata yonse ya zondeni yomwe alimi angalime.

Jedegwa adati kupatula kuti ndi chakudya, ufa wa mbatata ya zondeni ndi mankhwala othandiza kumatenda osiyanasiyana monga mtima, kuthamanga kwa magazi, shuga, zilonda zam’mimba ndi kuphwanya kwa minofu.

Iyi ndi mbewu ina yomwe msika wake wapezekeratu kuwonjezera pa mbewu zamtundu wa nyemba zomwe kampani ya Auction Holdings Commodities Exchange idalimbikitsa alimi kuti abzale poti msika wake ulipo kale. n

Related Articles

Back to top button
Translate »