Nkhani

Msonda: Tsamba loyoyoka mu PP?

Listen to this article

Nthawi yomwe anthu akuchoka m’chipani cha Peoples Party (PP) chitangogwa m’boma, mneneri wa chipanichi, Ken Msonda, yemwe ali ndi lilime lakuthwa komanso amayankhula mokhadzula, amawayerekeza anzawowo ngati masamba ouma amenene akuyoyoka m’mitengo nthawi ya chilimwe.

Lero zagwa pamphuno.

Wachoka mu PP: Msonda
Wachoka mu PP: Msonda

Kodi pano Msonda nditsamba louma limene lathothoka m’chipani chakale cholamula kuti zichitire ubwino chipanichi?

Wogwirizira utsogoleri wa PP, Uladi Mussa akuti Msonda, ngati wina aliyense, ali ndi ufulu wochoka mu chipanichi.

Msonda akunenetsa kuti iye ndi katakwe pandale ndipo kuchoka kwake m’chipanichi sikutanthauza kuti ukatakwe wake pandale watha, ayi, koma akumvera zimene Mulungu wake akumuyankhula.

Iye dzana Lachinayi adalonjedza kuti auza mtundu wa Malawi zifukwa zochokera m’chipanichi ndi zomwe akulingalira kuchita pamoyo wake mtsogolomu pamsonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre, koma dzulo, iye adasintha thabwa ndi kuuza atolankhani kuti msonkhanowu walepheleka atamvera malangizo a mbusa wake.

“Abusa anga andiuza kuti ndisapangitse msonkhano wa atolankhaniwu. Akuti ndidekhe kaye mpakana nthawi yoyenerera yokhazikitsidwa ndi Mulungu itakwana.

“Ndikupempha anthu kuti andimvetsetse. Monga mmene ndanenera kale, ndikufuna kuzamisa moyo wanga wa uzimu komanso kukhala ndi nthawi yokwanira ndi banja langa,” Msonda adatero.

Mkuluyu adati adayankhulana ndi mtsogoleri wa chipani cha PP, Joyce Banda—amene ali kunja kwa dziko lino komwe akhala chigonjereni pazisankho za mu 2014—za kuchoka kwake.

Msonda adati Banda adamupempha kuti asachoke msanga kufikira iyo atabwerera ku Malawi, koma idati izi sizikadagwirizana ndi chikonzero chake chopempha Mulungu kuti amutsogolere pa za tsogolo lake mundale komanso muuzimu.

Iye adati zomwe amayankhulira anzake powayerekeza ngati masamba ouma amene akuthothoka mumtengo nthawi ya chilimwe zidali gawo la ntchito yake potumikira chipani.

“Ngati mmeneri wa chipani, ndimayenera kuyankhulira chipani komanso kupereka chithunzithunzi chabwino cha chipanichi kumtundu wa Malawi. Koma izi sizikusonyeza kuti ine ndi tsamba louma lomwe latha ntchito.

“Poti ndanena kuti ndikufuna ndizame muuzimu kaye, za ine akambe ndi anthu. Ndale ndazisiya kale apo, koma mtsogolomu mundiona ndikuzapanga nawo mpikisano pachisankho cha aphungu a ku Nyumba ya Malamulo mu 2019,” Msonda adatero.

Mkuluyu, yemwe wakhala akusintha zipani komaso amadziwika kwambiri ndi dzina loti ‘Foot Soldier’, akuti panthawi yoyenera adzauza anthu dongosolo limene akupempha Mulungu kuti amukonzere.

Msonda, yemwe lilime lake lamuikako m’mavuto potengeredwa kukhoti atamemeza anthu kuti azipha anthu amene amagonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, adalowa mu chipani cha PP mu January 2012, chipanichi chisanalowe mboma koma mayi Banda ali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Bingu Wa Mutharika.

Iye adasankhidwa kukhala mneneri wa PP ndipo udindowu udapitirira chipani cha PP chitalowa m’boma potsatira imfa ya Bingu wa Mutharika.

Msonda, yemwe adakhalakonso wothandizira mmeneri m’chipani cha UDF asadalowe PP, wakhala akusowetsa mmtendere chipani cholamula ndi kuyankhula kwake kokhadzula, ndipo kumayambiriro a chaka chino, adauzapo mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti atule pansi udindo wake kaamba koti alephera kukonza vuto la zachuma ndi zina.

Izi anayankhula kumsonkhano wa anthu onse okhuzidwa wa Public Affairs Committee (PAC)mu mzinda wa Blantyre, ndipo kuyankhula uku kudakwiyitsa nduna zambiri zomwe zinkatenga nawo gawo kumsonkhanowu.

Chipani cha PP chakhala chikutaya atsogoleri ake ofunikira kwambiri kuphatizapo Sidik Mia, yemwe adatula pansi udindo wake ngati pulezidenti wothandizira m’chigawo cha kummwera chisankho za 2014 chitatsala pang’ono.

Ndipo chipanichi chitagwa pa zisankho za 2014, akuluakulu ena amene achoka m’chipanichi ndi Caeser Fatch, Stephen Mwenye, Tony Ngalande, Moses Kunkuyu ndi ena ambiri. n

Related Articles

Back to top button