Nkhani

Mswahara wa zifukwa

Munga wadza ndi mafinya omwe. Pamene ena akumwetulira kuti boma lakweza mswahara wa mafumu, mafumu ena ati kukwezaku kuwabweretsera mavuto pa ufumu wawo komanso ku boma.

Ndondomeko ya zachuma yomwe nduna ya zachuma yabweretsa, boma lati likweza malipiro a mafumu ndi 100 pelesenti ngati aphungu avomereze bajeti imene nduna ya zachuma Goodall Gondwe idapereka m’Nyumba ya Malamulo Lachisanu lapitalo.

Mswahara wa mafumu ngati awa aukweza

Malinga ndi ndondomekoyo, Paramount yemwe amalandira K50 000 kuyambira pa 1 July azilandira K100 000 pomwe ma Senior Chief malipiro awo afika pa K60 000 kuchoka pa K30 000 ndipo ma T/A azilandira K36 000 kuchoka pa K18 000. Magulupu omwe amalandira K5 000 tsopano afika pa K10 000 ndipo nyakwawa zimene zinali pa K2 500 zizilandira K5 000.

Mafumu ena ati izi ndi ndale zomwe zingagwetse mafumuwo. “Palibe vuto pokweza malipiro koma nkhani nkuti akukweza pano bwanji?” yadabwa mfumu ina m’boma la Mwanza.

“Kuyambira pamene DPP idalowanso m’boma mu 2014, takhala tikuwapempha kuti atikwezere mswahara. Panalibe chisonyezo choti atikwezera, pano pamene nthawi ya kampeni yayandikira akukweza mswahara uja. Zachitika pano chifukwa chiyani?”

Mfumuyo ikuganiza kuti boma lapanga dala zowakwezera malipiro awo lero cholinga ‘tithandize chipani posaloleza otsutsa kuchititsa misonkhano m’madera athu kuti DPP ilowenso m’boma.”

Mneneri wa chipani chotsutsa cha MCP, Maurice Munthali adati kukweza kwa malipirowo si nkhani koma pawadabwitsa ndi nthawi yomwe izi zikuchitika.

“Zikuonetseratu kuti iyi ndi nyambo yopangira kampeni. Izi ndi zomwe mtsogoleri wotsutsa Lazarus Chakwera adanena kale kuti ndondomeko iyi ndi yakampeni,” adatero Munthali.

Mneneri wa boma Nicholas Dausi adati nthawi ino si yakampeni kotero malipiro a mafumu alibe kampeni kumphasa.

“Mafumu omwewo amadandaula, lero boma tawaganizira, ndiye talakwanso? Timvera kwa mafumuwo ngatidi talakwa,” adatero Dausi.

Nyakwawa ina ya m’boma la Ntcheu idati ili ndi tanthauzo kwa mafumuwo kuti alowe chipani cholamula. “Apatu ndiye kuti tingolowa DPP nanga n’kutaninso?”

Mu 2005 Bingu wa Mutharika atakweza malipiro a mafumu, zidamuthandiza kuti chisankho cha 2009 apambane mokokoleratu mavoti m’zigawo zonse kugwetsa John Tembo yemwe amatsogolera chipani cha MCP.

Mbali ina yomwe mafumuwo akuopa ndi ufumu wawo kuti kukhala nkhondo kumenyana ndi abanja kuti ena atenge ufumu wawo.

“Nkhondo ndi yosayamba, abanja amene sukugwirizana nawo ayesera kumenya nkhondo kuti alande ufumu poona kuti uli ndi ndalama zambiri.

Angalole ndani kuti K100 000 imuphonye pamene iye alibe chochita?” akuganiza choncho.

Koma Senior Chief Mabulabo Jere ya m’boma la Mzimba yati apa palibe choopsa chifukwa mafumu amagwira ntchito yambiri ndipo kukweza kwa malipiroko sikuti kwabwera ndi zifukwa.

“Kodi pali ndalama zoti mpaka munthu angachite nazo mantha apapa? Taganizani ntchito yonse zimagwira nyakwawa zija koma pakutha pa mwezi kulandira K2 500,” adatero.

Koma kadaulo pa nkhani ya ulamuliro wabwino Henry Chingaipe wati ngakhale iyi ili nkhani yabwino, komabe pafunika kuzukutira bwino chifukwa malipirowo akuoneka kuti ndi azifukwa.

Related Articles

Back to top button