Nkhani

Mswati adakali mfumu—Boma

Listen to this article

Boma, kudzera mwa mneneri wa unduna wa maboma aang’ono ke Muhlabase Mughogho, lati ngakhale pali kukokanakokana pa ufumu wa Gomani V, boma likuvomerezabe Mswati Gomani wachisanu kuti ndiye mfumu.

Mughogho adanena izi pamene mbali ina ya banja la Gomani motsogozedwa ndi Dingiswayo yalengeza kuti Dingiswayo ndiye mfumu, kulanda ufumuwu kwa Mswati.

Gomani V
Gomani V

Lachiwiri akuluakulu ena abanja adatsutsa zomwe Dingiswayo adalengeza kuti Mswati adakalibe mfumu. Koma patangodutsa tsiku abanjawa atalankhula, Dingiswayo adachititsanso msonkhano wa atolankhani kuti zomwe adanena abanjawa ndizabodza ndipo iye ndiye mfumu yatsopano.

“Panopa ofesi ya Gomani yasamuka kuchoka ku Lizulu ndipo tikulankhulamu ili kwa Nkolimbo,” adatero Dingiswayo.

Koma malinga ndi Mughogho, Mswati ndiye mfumu. “Boma likudziwa Mswati kuti ndiye mfumu, izi zili choncho chifukwa mfumu ikasankhidwa ndi abanja, boma limavomereza ndipo mwambo udachitika wodzoza Mswati kukhala Gomani wachisanu. Izi sizidasinthe mpaka lero.”

Gawo 11 (1) la malamulo okhudza mafumu, Chiefs Act la m’chaka cha 2000 limati pulezidenti wa dziko ndiye ali ndi mphamvu yochotsa Paramount Chief, Senior Chief, Chief komanso Sub Chief.

Mswati adadzozedwa mu pa August 10, 2012 kukhala Gomani wachisanu kutsatira imfa ya bambo ake.

Azakhali ake Rosemary Malinki ndiwo akhala akugwirizira ufumuwu pamene amadikira kuti Mswati akule kaye asadamulongwe ufumuwo. n

Related Articles

Back to top button