Nkhani

Mtambo walowa ndale

Listen to this article

Yemwe adali wapampando wa gulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) Timothy Mtambo wati wasintha nthabwa ndipo pano wayamba ndale zenizeni.

Mtambo wati waganiza zoyamba ndale ndipo wati cholinga chake chachikulu n’kuthandizira mgwirizano wa zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party kuchotsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wa Democratic Progressive Party (DPP) pampando.

Mtambo kulankhula pazionetsero zina mmbuyomu

Iye wayambitsa gulu la ndale lomwe silidafike pa chipani ndipo akulitcha Citizens for Transformation (CFT) ndipo wati ndi wokwiya kwambiri ndi momwe chipani cha DPP chasokonezera dziko la Malawi.

“Ndakhala ndikulingalira za dziko lino kuyambira pomwe tidapeza ufulu wa demokalase mu 1994 ndipo ndaona kuti dziko lathu laonongeka kwambiri chifukwa cha ulamuliro wopanda masomphenya,” adetero Mtambo polengeza zakutembenuka kwake Lachitatu ku Lilongwe.

Kadaulo pa ndale George Thindwa wati ngakhale Mtambo wasiya anzake padzuwa, iye watembenuka nthawi yabwino chifukwa akhonza kukwaniritsa zolinga zake mosavuta komanso mosadikira nthawi yaitali.

“Ngati mwamumvetsa, akuti akufuna kuthandizana ndi mgwirizano wa MCP ndi UTM kuchotsa Mutharika pampando. Masomphenya awa ndi nthawiyi walondola chifukwa ngati amapanga za mseri, tsopano amasuka,” watero Thindwa.

Pogwirizana naye, kadaulo wina Mustafa Hussein wati Mtambo wachita bwino chifukwa wayamba ndale ataona kale momwe ndalezo zimakhalira ndiye sakavutika kukwaniritsa zolinga zake.

“Mtambo wakhala akutsogolera zionetsero zosiyanasiyana m’dziko muno ndipo wakumana ndi zambiri pantchitoyi. Iyeyu ali ngati wandale kale yemwe wakumana ndi zokhoma ndiye waganiza bwino,” watero Hussein.

Naye kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko Makhumbo Munthali wati ngakhale pakhonza kukhala mafunso pa ganizo la Mtambo losiya kutsogolera HRDC, zolinga zake sizikadakwaniritsidwa akadakakamira ku gululo.

“Ali ndi zolinga zomveka koma sakadazikwanitsa akadakhala ku HRDC. Iyeyu amayenera ndithu kukhala paufulu ngati wandale ndithu mpomwe zimuyendere bwino. Ife timuika m’mapemphero kuti akwaniritse zofuna zake,” watero Munthali.

Akadaulo atatuwa agwirizananso pa mfundo yoti kuchoka kwa Mtambo sikungasokoneze gulu lonse chifukwa mapulogalamu onse a bungwe amapangira limodzi ndi anzake omwe wawasiya ndiye iwowo apitiriza pomwe iye wasiyira.

Koma nduna ya zachitetezo cha m’dziko Nicholas Dausi ndi nduna ya zofalitsa nkhani Mark Botoman ati sakudabwa kuti Mtambo wabwera poyera ndi ndale chifukwa iwo adadziwa kale kuti mkuluyu ndi wandale.

“Asatiphimbe m’maso kuti lake ndi gulu chabe ayi koma kuti ndi chipani cha ndale. Ganizo lake silalero ndipo labwera ngati chithokozo kuchipani cha MCP ndipo muona amupatsa mpando waukulu kuchipani,”adatero Dausi.

Related Articles

Back to top button