Chichewa

Mthirira usathere panjira

Listen to this article

Kaitane Shuga wa m’mudzi mwa a Gavi ku Chileka m’boma la Blantyre ndi mmodzi mwa alimi amene amachita ulimi wothirira koma kusiyana ndi chaka chatha, iye akuti padakalipano zitsime zimene amapezapo madzi zayamba kuphwa.

Iye ali ndi nkhawa kuti mbewu zimene wabzala kachiwiri zikhonza kupserera zisadache kaamba kakusowa kwa madzi.

“Padakalipano ndafukula kale zitsime zanga ndipo ndikumachita kudikirira kuti madzi abwerepo ndiyambe kuthirira pamene chaka chatha ndidalima kokwana katatu osakumana ndi vuto limeli kufikira madziwa adafika ndi nyengo ya mvula,” adadandaula motero.

Naye Eneless Timothy wa m’boma la Chikwawa akuti mtsinje umene iye pamodzi ndi alimi anzake a m’deralo amapatutsako madzi ndi kumathirira mbewu zawo achepa.

Sungani madzi othirira mbewu kuti mupindule ndi mthirira

Zotsatira zake, sakubwera ndi mphamvu choncho mbewu zimene zili kumtundako pang’ono sizikupeza madzi.

“Timagwiritsa ntchito makhwawa ndipo madzi akachepa amayenda mofooka. Izi zikupereka chiopsezo choti akhoza kuphwereratu,” iye adatero.

Malingana ndi katswiri wa zaulimi wothirira ku nthambi ya zakafukufuku wa za ulimi m’dziko muno Isaac Fandika, mvula ikagwa yocheperapo, malo osungira madzi amene amadziwika kuti water table m’Chingerezi amatsika.

Zotsatira zake, anthu makamaka alimi amene amachita ulimi wothirira amakanika kufikira madziwa koma iye adafotokoza kuti alimi akhoza kuchepetsa vutoli pochepetsa kagwiritsidwe ntchito kamadzi pothirira mbewu.

Katswiriyu adafotokoza kuti alimi akhoza kuchepetsa kagwiritsidwe ntchito ka madzi pophimbira mbewu, kuthirira mbewu madzi ocheperapo kapena kugwiritsa ntchito mthirira wosunga madzi wongodonthetsera pa mbewu umene umadziwika kuti drip irrigation pa chizungu.

“Mlimi akaphimbira mbewu ndi mapesi pamene akuchita ulimi wothirira, amathandiza kuti madzi asamauluke kuchoka m’nthaka kupita m’mwamba mwansanga. Zotsatira zake, amakhalitsa m’nthaka kwa nthawi yaitali choncho mlimi sathirira pafupipafupi.

“Izi zimathandiza kuti malo amene mlimi akupeza madzi othiririra mbewu zake mwachitsanzo pachitsime, padamu kapena mumtsinje akhalitse chifukwa amakhala ngati wasungako ena,” iye adatero.

Fandika adafotokoza kuti kuchepetsa madzi othirira mbewu ndi njira imene mlimi amadumpha makhwawa ena osawathirira ndipo ulendo wina n’kudzawathirira kwinako akudumpha makhwawa amene adathirira mmbuyomo koma osachepetsa zokolola.

Iye adati njirayi imathandiza kupulumutsa kapena kusunga madzi amene adakathiriridwa m’makhwawa kapena kuti m’makanalo enawo choncho zimamupatsa mlimi mwayi wogwiritsa ntchito madziwa kwa nthawi yaitali.

Fandika adati mthirira wongodonthetsera madzi pa mbewu ndiwodalirirka kwambiri pa nkhani yoteteza kutayika kwa madzi ku ulimiwu.

Malinganana ndi wachiwiri kwa mkulu woona za ulimi wothirira m’dziko muno Geoffrey Mwepa, mthirira wa mtunduwu umachepetsa kutaika kwa madzi ndi pafupifupi magawo 80 mwa 100 aliwonse.

“Izi zili chomwechi chifukwa mthirirawu umadonthetsera madzi okhawo ofunikira pa mbewu mosapyola muyeso komanso popanda kuthira malo osafunikira mwachitsanzo munda wonse,” adafotokoza motero.

Mphunzitsi wa ku nthambi ya zaulangizi ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Paul Fatch adaonjeza kuti kubzala mitengo kuzungulira malo amene mlimi amapezako madzi othiririra mbewu kumathandiza kuti malowa asaphwe msanga.

Iye adati izi zili chomwechi chifukwa imateteza madzi kuti asamauluke kwambiri kupita m’mwamba.

Related Articles

Back to top button
Translate »