Nkhani

‘Mtima pansi, makuponi akubwera’

Boma lati anthu omwe chiyembekezo chawo chili pazipangizo zaulimi zotsika mtengo za sabuside, asataye mtima ndipo achilimike kukonza mminda mwawo kaamba kakuti makuponi ogulira zipangizozi afika sabata ikudzayi Lolemba.

Chilimbikitsochi chadza pomwe anthu adali ndi nkhawa kuti mvula yayandikira komanso madera ena yagwa kale mwa ndii koma tsogolo la makuponi ogulira zipangizo silimaoneka bwinobwino.

Fisp fertiliser and seed will be handled by private traders this year
Fisp fertiliser and seed will be handled by private traders this year

Mvulayi yagwa m’madera ena m’zigawo zonse kuyambira sabata zitatu zapitazo ndipo pomwe anthu ena ali jijirijijiri m’minda mwawo, anthu ena amadandaula kuti mwina mwayi wogula zipangizozi ukhoza kudzafika mmera utakwinimbira.

“Si zongoganiza ayi, taziwonapo mmbuyomu kuti pomwe zipangizo zikufunika, kumisika kulibe kapena makuponi sadafike ndiye umayamba ntchito n’kudzakhumudwa pambuyo,” adatero Ammon Yesani Bakulo, mmodzi mwa alimi omwe akuyembekezera kulandira nawo makuponi kwa Chiseka m’boma la Lilongwe chaka chino.

Koma nduna ya zaulimi, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, wati nkhawayi njopanda mtsitsi kaamba koti mkati mwa sabata ikudzayi, makuponi ayamba kufika ndipo azigawidwiratu.

“Ndikunena pano, makuponi adindidwa kale moti sabata yamawayi akhala akufika ndipo nthawi yomweyo azigawidwa kuti anthu ayambe kugula zipangizo. Sitikufuna kuti munthu adzadandaule patsogolo, ayi,” adatero Chaponda.

Mndondomeko ya chaka chino muli kusintha kungapo komwe Chaponda wati kuthandiza kupititsa patsogolo cholinga cha pologalamu ya sabuside.

Kwina mwa kusinthaku ndi kukhazikitsa mitengo yatsopano ya makuponi, kutsitsa chiwerengero cha anthu omwe apindule mupologalamuyi, komanso kupereka kontirakiti kwa makampani abizinesi kuti agulitse nawo zipangizozi.

“Kubwera kwa makampani abizinesi ndi kumodzi mwa kusintha komwe kuthandize kwambiri ndipo kupangitsa kuti zipangizo zotsika mtengo zizipezeka pafupi ndi anthu komanso chifukwa cha mpikisano, mitengo isanyanye poti aliyense azifuna kugulitsa,” adatero Chaponda.

Mupologalamu ya chaka chino, mtengo wa kuponi ya feteleza wokulitsa ndi wobereketsa uli pa K15 000 pomwe mbewu za chimanga papaketi ya 5kg kuponi yake ili pa K5 000 ndipo mbewu zamtundu wa nyemba zolemera 2kg mpakana 3kg kuponi yake ili pa K2 500.

Chaponda adati mitengoyi ndi yomwe boma likuwonjezera pa mlimi, osati mitengo yogulira kumsika.

“Mwachitsanzo, ngati thumba la feteleza lili pa K18 000, ndiye kuti boma laperekako K15 000 ndipo K3 000 yotsalayo apereke ndi mlimi,” adatero Chaponda.

Malingana ndi malipoti a zanyengo, chaka chino, mvula ikhoza kugwa bwino moti unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi ukulimbikitsa alimi kuti alimbikire ntchito za m’minda.

Related Articles

Back to top button