ChichewaEditors Pick

Mtima pansi, mayeso A jce alipo chaka chino

Listen to this article

 

Ngati panali kupeneka kulikonse kuti chaka cha 2015/16 kukhala kapena sikukhala mayeso a Junior Certificate of Education (JCE) kutsatira zomwe boma lidalengeza posachepadwa kuti lathetsa mayesowo m’sukulu za sekondale, kukaikako kutheretu chifukwa boma latsimikiza kuti mayesowo alembedwa.

Eni sukulu zomwe si zaboma akhala akudandaula kuti boma lawaika pachingwe cha kangaude polephera kubwera poyera ndi kufotokoza ngati mayesowo aliko kapena ayi zitangomveka kuti boma lathetsa satifiketi ya JCE, koma osamasula kuti zimenezi ziyamba liti.

Ophunzira kulemba mayeso a JCE mmbuyomu
Ophunzira kulemba mayeso a JCE mmbuyomu

Mneneri wa unduna wa zamaphunziro, Manfred Ndovi, wati pasakhale mpungwepungwe uliwonse pankhaniyi poti mayesowa aliko koma kuyambira chaka cha mawa cha 2017 mayesowa sadzalembedwanso.

“Mayeso aliko! Chaka chino chikhala chomaliza kulembetsa mayeso a JCE koma kuyambira chaka cha 2017 sikudzakhalanso mayeso oterewa,” adatero Ndovi pouza Tamvani palamya.

Iye adati sukulu ndi ana onse omwe ali Fomu 2 ndipo akuyembekezera kulemba mayeso a JCE, atsatire ndondomeko zonse zoyenerera pokonzekera mayesowa, osati kutekeseka.

Mkulu wa bungwe la eni sukulu zomwe si zaboma, Joseph Patel, adauza Tamvani kumayambiriro a sabatayi kuti eni sukuluzi akusowa kolowera pankhaniyi kaamba kakuti sakudziwa ngati mayesowa alembedwe chaka chino kapena ayi.

Boma lidaganiza zoyambitsa njira yosefera ophunzira potengera momwe akuchitira m’kalasi komanso pamayeso a teremu iliyonse m’makalasi onse kulekeza Fomu 3 kuti Fomu 4 ndiyo azilemba mayeso a boma.

Pofotokoza mmene zizidzayendera, nduna ya zamaphunziro, Dr Emmanuel Fabiano, idauza Tamvani kuti ndondomeko yatsopanoyi ikadzayamba bungwe la Maneb lidzasamba m’manja pachilichonse chokhudza JCE ndipo malo olemberamo mayeso (cluster centres) ndiwo adzasenze udindo.

“Ndondomeko idzakhala yakuti malo olemberamo mayeso ndi ana omwe akuyenera kulemba mayeso azidzalipira ndalama za mayeso ku ‘cluster’ yomwe izidzakonza mayeso ndi kulembetsa,” adatero Fabiano.

Ndunayi idati sipadzakhala zobwereza kalasi kapena kuchotsedwa—okhoza ndi olakwa omwe azidzapitirira mpaka mu Fomu 3.

Fabiano adati boma lagani izi pofuna kupereka mpata kwa ophunzira onse omaliza nawo maphunziro a kusekondale komwe akalemba mayeso a Fomu 4, okhoza azidzapatsidwa satifiketi ya MSCE pomwe olakwa azidzalandira kalata yaumboni yoti adamaliza maphunziro a kusekondale.

Iye adati izi zizichititsa kuti ambiri azilandira nawo maphunziro okwanira chifukwa mundondomeko yakale, olakwa JCE amachoka pasukulu ndipo ambiri sankakhalanso ndi chidwi chokapitiriza kwina.

Mfundo ya boma pochotsa mayeso a JCE ndi yakuti satifiketiyi idatha mphamvu chifukwa olemba ntchito ambiri masiku ano safuna satifiketiyi koma yokwererapo.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »