Nkhani

Mtsutso pa zoika a Covid-19

Kusamvana kukupitirira pakati pa achipatala ndi anthu pa ndondomekoyoyenera kutsatidwa munthu yemwe amadwala matenda a Covid-19 akamwalira.

Pomwe achipatala akuti munthu wodwala matendawa, achipatalawa amakonza thupili kuti lisapereke matenda kwa ena komanso kulilongeza m’thumba loyenera pamaso pa achibale, athu ena atsutsa kuti sakhala nawo poonelera ntchitoyi.

Achipatala kuika maliro a Covid

Mmodzi mwa a zaumoyo ogwira ntchito pa chipatala cha Bingu National Stadium (BNS), Gloria Guzani adauza mtundu wa Amalawi mkati mwa sabatayi pamsonkhano wodziwitsa anthu za momwe matendawa akuyendera m’dziko muno omwe umachitika tsiku lililonse mumzinda wa Lilongwe kuti anthuwasakuyenera kutsekula thumbali chifukwa munthu akhonza kutengabe matendawa kudzera m’timadzi tina totuluka mkamwa, mphuno komanso malo ena a thupi.

Koma Guzani atangonena izi, mtsutso waukulu udabuka pa masamba amchezo osiyanasiyana onena kuti Guzani akunama chifukwa achipatalawasamavomereza kuti achibale awonerere nawo mwambo wokonza thupi.

Mmodzi mwa anthuwo Emily Botomani adanenetsa kuti Guzani adalinamizadziko chifukwa iye adataya mayi ake ku matendawa mwezi watha ndipoadangolandira mtembo.

“Ndinkafuna kuwaona mayi anga wokondedwa komaliza, koma izisizidatheke, mwina kwa ena zimachitika, koma ine sizidachitike ndipondidangokhala panja kudikilira thupi,” adalemba motero Botomani.

Ndipo winanso Chester Chibwe adavomereza kuti naye mbalewake atamwalira sadakaonelere nawo mwambo wokonza thupi.Pomwe winanso Chisomo Ntaba Nkhata adatsutsa zomwe achipatalawa adanenazo.

Ena mwa anthuwo adapitirira kupempha boma kuti lizipereka thupi kwaachibale kuti azikasunga okha popeza limakhala laikidwa kalem’makhwala ndipo chiopsezo chopereka matenda a Covid-19 chimakhalachotsika.

Ndipo enanso adafunsa kuti boma liwauze zifukwa zomveka bwino zomweakutengera mtembo wa Coronavirus ngati wa matenda a Ebola.

Ndondomeko zovomerezeka zoikira malirowa zimanena momveka bwino kutiachipatala kwawo ndi kukonza thupi kuti lisapereke matenda ndipo akhoza kuwalekera a banja kukasunga okha thupi ataphunzitsidwa bwino.

Komatu tikuonabe achipatala ambiri akuika thupi zomwe zikumautsamapokoso pakati pa achipatalawa ndi mabanja oferedwa makamaka maderaa kumudzi.Izitu zachititsa achipatala ena kumenyedwa mpaka kuvalazidwam’midzi pokaika maliro.

Posachedwapa tidaona dalaivala wa chipatala cha pa Kasunguatavulazidwa. Ku Machinga, izi zidachitikanso chimodzimodzi m’boma la Dowa.

Malinga ndi mkulu wa pachipatala chachikulu cha Mzuzu, Frank Sinyiza,anthu a zaumoyo tsopano akumanyinyirika kukaika maliro poopa zipongwe zomwe anzawo akuchitiridwa m’midzi.

“Pakadalipano tikumangowauza kuti apeze okha mayendedwe ndipo tikumawapatsa thupi ndi kuwalumikizitsa ndi a zaumoyo omwe ali m’dera lomwe akukasunga thupilo. Chiyambireni kupanga izi, sitidamveponso madandaulo alionse,” adalongosola Sinyiza.Pa nkhani yokonza thupi, Sinyiza adati achipatala akakonza thupi ndi mankhwala akupha tizirombo, amaitana abale kuti akhale pomwepo akamaika m’thumba kuti aonerere zonse.

“Katundu wa malemunso timamuika m’mankhwala opha tiziromboti ndipoabale ena amatiuza kuti tikaotche pamene ena amamutenga,”adalongosola motero.Polankhulapo, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe oona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mehn) George Jobe adati mmene zinthu zilili zaziwawaachipatala asiye zomakaika maliro a munthu womwalira ndi matenda a

Covid 19 komanso asiye zotengera thupi muambulansi zawo.“Chofunika n’kuwaphunzitsa abale osati pakamwa pokha komanso kuwalembera ndithu papepala m’chilankhulo chawo ndondomeko zoyenera kutsatira pokasunga thupilo,” adatero Jobe.Iye adatinso m’zipatala zomwe akhala akuyendera, achipatala amaitana anamfedwa kukaonera mwambo wokonza thupi kunyumba zachisoni.

“Koma popeza sitidayendere madera onse, n’zotheka kuti mwina kwina sakutsatiradi ndondomekoyi. Koma ili likhale phunziro kwa achipatala onse kuti abale azikhalapo ndithu pokonza thupi osati mmodzi komaawiri,” adatero Jobe.

Related Articles

Back to top button