Chichewa

‘Mtumiki wa Mulungu adalosera’

Listen to this article

 

Onse okhulupirira amadziwa kuti zodzera m’manja mwa Mulungu n’zodalitsika ndipo zimayenda moyera monga momwe zikuyendera pakati pa mthutha wa chikopa Elvis Kafoteka ndi Thokozani Mazunda.

Awiriwa akuti adakumana m’chaka cha 2012 kumapemphero kutchalitchi cha Revival Church of All Nations ku Ntcheu, koma n’kuti mneneri wa Mulungu kumeneko, Themba Jere, atalosera kale kuti chisadafike chaka cha 2016, Thoko adzakhala atakumana ndi wachikondi wake.

Elvis akuti awiriwa atakumana mu 2012, adayamba kucheza ngati munthu ndi mnzake, osaganizirana kuti maganizo a wina ngotani, kufikira mu December m’chaka cha 2015 pomwe iye adafunsira namwaliyo.

Thokozani ndi Elvis patsiku la chinkhonswe
Thokozani ndi Elvis patsiku la chinkhonswe

“Mmene tinkakumana tidali tisakudziwana koma tidakhulupirira kuti mphamvu ya Mulungu idalipo chifukwa tidayamba kucheza ngati anthu oti tidadziwana kalekale. Tidapitiriza choncho mpaka 2015 pomwe ndidamufunsira ndipo adandivomera,” adatero Elvis.

Iye akuti panthawi yonseyi, Thoko ankamubisira za masomphenya a mneneri Jere ndipo pa 31 December 2015 kuti mawa lakelo ndi 2016, awiriwa adakumana kumapemphero a usiku komwe adafunsirana.

“Mwina samandiuzira dala kuti aone zotsatira za masomphenya a mneneriyo. Patsikulo kudali kuti mawa lake 2016 wafika ndipo ndimakhulupirira kuti mphamvu ya Mulungu idagwirapo ntchito kwambiri,” adatero Elvis.

Pa 4 June awiriwa adapanga chinkhoswe kunyumba kwa a Loga m’boma la Ntheu ndipo pologalamu yaukwati idakonzedwa kuti udzakhaleko pa 3 June chaka chamawachi.

Iye adati amakonda chilichonse pamoyo wa Thoko monga momwe naye Thoko akuti amakondera Elvis.

Elvis amachokera m’mudzi mwa Zenga, T/A Khongoni m’boma la Lilongwe, pomwe Thoko amachokera m’mudzi mwa Mankhamba, T/A Tomasi, m’boma la Thyolo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »