Nkhani

Mtunda ulipo pa zokambirana

Listen to this article

Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bakili Muluzi sali kutali kwenikweni ndi khumbo lake lofuna kukumana ndi atsogoleri a Human Right Defenders Coalition (HRDC) pa nkhani ya zionetsero koma atsogoleriwo ampatsa mtunda woti akwere izi zisadatheke.

Mwa zina, Muluzi akuyenera kukambirana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika, wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah, bungwe la Public Affairs Committee (PAC) ndi atsogoleri a zipani zina za ndale kuti adzakhale nawo pa zokambiranazo.

Akufuna mkumano: Muluzi

Muluzi adalembera kalata atsogoleri a HRDC pa 19 August 2019 kuwapempha kuti akumane n’kukambirana pa chikonzero cha HRDC chofuna kupanga chionetsero m’zipata za dziko ndi mabwalo a ndenge kuyambira pa 26 mpaka 30 August.

M’sabata ikuthayi, iye adapempha kuti mkumanowo utakhalapo dzulo kapena lero lino zingathandize chifukwa zionetserozo zomwe zikuyembekezeka kuyamba Lolemba zikhala zisadachitike.

“Pofunira zabwino dziko lathu, ndikupempheni kuti bwanji tikumanenso n’kukambirana nkhani ya zionetseroyi. Ndikuona ngati njira yabwino yothanirana ndi mavuto omwe ali m’dziko lathuli nkukhala pansi,” adatero Muluzi m’kalatayo.

Ndipo poyankha kudzeranso m’kalata, bungwe la HRDC lati Muluzi adalephera kukwaniritsa pangano lake ndi bungwelo utatha mkumano woyamba omwe udachitika pa 23 July 2019.

“Choyamba mudatilonjeza kuti mukumana ndi Mutharika komanso Ansah ndipo mutiuza zomwe mukambirane naye pasadathe sabata imodzi koma mpaka pano sitidamve kanthu ndiye kukukhulupirirani kuvuta,” yatero kalata ya HRDC.

Kalatayo yapitiliza kuti mkumanowo kuti utheke, Ansah atule pansi udindo yekha kapena Mutharika yemwe adamusankha amuchotsepo ndipo izi zifalitsidwe kudzera m’nyumba zofalitsa nkhani kuti anthu m’dziko lonse adziwe.

Malingana ndi momwe yalembedwera kalata ya HRDC, zikutanthauza kuti Muluzi akapanda kukwaniritsa zinthuzi, mkumano ndi HRDC walephereka.

Koma katswiri pa ndale George Phiri wati iyi si ntchito yamasewera kwa Muluzi ndipo wati n’zokaikitsa kuti akwanitsa kubweretsa mbali zonsezi pamodzi.

“HRDC yanena za nzeru chifukwa zokambirana zimayenera kukhala

olimbanawo pomwepo, m’khalapakati pomwepo komanso ena okhudzidwa ndi wothandizira mkhalapakatiyo pomwepo koma sindikuona izi zikutheka,” adatero Phiri.

Kadaulo winanso yemwe amaphunzitsa za ndale ku Chancellor College, Mustafa Hussein, wagwirizana ndi milingo yomwe HRDC yapereka kwa Muluzi polingalira kuti adalephera kale poyamba.

“Poyamba HRDC idali ndi chiyembekezo choti Muluzi auza Amalawi zomwe adakambirana ndi Mutharika koma adasankha kusunga chinsinsi. Muluzi abweretse pamodzi Mutharika, Ansah ndi HRDC,” adatero Hussein. n

Nkhani yokwenza mtengo wa chimanga nd iyabwino, koma yadza nthawi yolakwika alimi ambiri atagulitsa kale chimanga chawo kwa mavenda.

Awa ndi maganizo a alimi osiyanasiyana omwe adacheza ndi Tamvani patatha sabata imodzi unduna wa malimidwe utalengeza kuti mtengo omwe bungwe la Admarc lizigulira chimanga wasintha.

Nduna ya zamalimidwe Kondwani Nankhumwa adalengeza Lachisanu kuti kuyambira sabata yatha, mtengo wa chimanga wakwera kuchoka pa K150 pa kilogalamu kufika pa K180 pa kilogalamu Admarc ikakagulira chimanga kumudzi ndipo K200 pa kilogalamu mlimi akapititsa yekha chimanga ku msika wa Admarc.

Koma pocheza ndi Tamvani, alimi ena ati ngakhale nkhaniyo ili yabwino, palibe chomwe alimi ang’onoang’ono apindulepo chifukwa adagulitsa kale chimanga kwa mavenda pa mitengo yotsikirapo yomwe panthawiyo inkaoneka yabwino.

Mmodzi mwa alimiwo, William Guza wa ku Waliranji m’boma la Mchinji ndipo awa ndi madandaulo amene amakhalapo chaka chilichonse.

“Chaka ndi chaka timadandaula nkhani yomweyi kuti Admarc imachedwa kuyamba kugula chimanga ndipo ikamabwera m’bwalo, mavenda amakhala atagula kale chimanga m’midzimu  motola mapeto ake mavendawo ndiwo amakapindula pokagulitsa chimanga chomwecho ku Admarc,” adatero iye.

Moses Kawodzera mlimi wa ku Chisi m’boma la Zomba naye wati Admarc ikadayamba kugula chimanga pa mtengo watsopanowu nthawi yabwino, iye akadapeza phindu lokwana kawiri lomwe adapeza chifukwa chogulitsa kwa mavenda.

“Panthawiyo, mavenda adayamba kugula chimanga pa mitengo ya pakati pa K70 ndi K100 pa kilogalamu pomwe boma lidali lisadayambe kugula chimanga,” adatero Kawodzera.

Izi zikutanthauza kuti alimi omwe adagulitsa chimanga chawo moyambirira, adaluza ndalama zokwana K100 kapena K120 pa kilogalamu iliyonse yomwe adagulitsa kwa venda.

Apa ndiye kuti mlimi yemwe adagulitsa matumba 20 a makilogalamu 50 lililonse pa mtengo wa K80 pa kilogalamu, adagulitsa makilogalamu okwana 1 000 nkupeza K80000 koma akadagulitsa chimangacho ku Admarc panopo pa K200 pa kilogalamu akadapeza K200 000.

Katswiri pa za malimidwe Tamani Nkhono Mvula adati iyi ndi nkhani yomvetsa chisoni chifukwa venda ndiye amapeza phindu lomwe mlimiyo akadapeza ndipo mlimiyo amangokhala pamodzimodzi osasuntha.

“Ichi n’chifukwa chomwe ndimanenera kuti Admarc imayenera kukhala ndi ndalama ukamafika mwezi wa March kuti alimi akangoyamba kukolola, izitsegula misika yake. Izi zikhoza kuthandiza kuti mavenda atsatire mitengo ya boma pofuna kulimbirana chimanga ndi Admarc,” adatero Mvula.

Maganizo a Mvula akugwirizana ndi lipoti ya bungwe la Civil Society Agriculture Network (Cisanet) lomwe lidati ndale za msika wachimanga zimapweteka alimi ang’onoang’ono nkumatukula mavenda.

“Mavenda amabwera n’kudzagula chimanga chifukwa Admarc ikuchedwa koma alimi akufuna ndalama msanga. Admarc ikamayamba kugula chimanga pa mtengo ikwera, chimanga chimakhala ndi mavenda omwe amapindula.

“Nkhanza siyithera pomwepa, njala ikayamba, alimi omwe aja amadzagula chimanga ku Admarc mokwera chifukwa Admarc idagula kwa mavenda mokwera ndiye nayo ikufuna ipezepo phindu pang’ono pokha,” likutero lipoti la Cisanet.

Izi zikugwirizana kwatunthu ndi momwe zakhalira chaka chino chifukwa alimi adagulitsa chimanga pa mtengo wa K80 pa kilogalamu kwa venda yemwe akukagulitsa pa mtengo wa K200 pa kilogalamu ku Admarc ndipo mlimi yemweyo adzayenera kugula chimangacho ku Admarc pa mtengo osachepera K200 pa kilogalamu.

Pano mtengo wachimanga wayamba kale kukwera mosalingalira za mavuto a zachuma moti m’madera ambiri thumba la makilogalamu 50 lili pa K12 000 koma m’madera ena monga ku Chikwawa lafika pa K14 400 pomwe ku Machinga ena akugulitsa pa K18, 000.

Mkulu wa bungwe la Cisanet Pamela Kuwali wati boma lachita bwino kukwenza mtengo wa chimanga koma lionetsetse kuti pali chilungamo pa kagulidwe kake kuti alimi ang’onoang’ono apindule nawo.

Related Articles

Back to top button
Translate »