Chichewa

‘Mudali mu basi ya National’

Listen to this article

Shamuda Drake ndi mtolankhani wa wailesi ya Galaxy yemwe tsopano ali pabanja ndi mkazi wake Madalitso Moyo. Momwe Drake amayamba ulendo wake wochokera ku Lilongwe komwe amakaona mchimwene wake kupolisi ya Kawale, sadadziwe kuti n’kupeza nthiti yakeyo.

Naye Madalitso, pamene amachoka ku Dwangwa komwe amagwira ntchito kukampani yopanga shuga ya Illovo ulendo wa ku Mzuzu kukaona abale patsiku lokumbukira anthu amene adafera ufulu wa dziko lino pa 3 March, samadziwa kuti n’kupeza wachikondi.

Drake ndi Mada adamangitsa ukwati ku Mzuzu

Awiriwa adakhala mpando woyandikana mubasi ya National Bus Company koma sanayankhulitsane, kufikira pamene adafika pamalo ochita chipikisheni apolisi a Matete.

“Apa mpamene tidayamba kulankhulana ndipo adandifotokozera komwe amalowera. Macheza adapitirira ndipo titafika pa Bandawe, ndidamufunsa ngati angandipatse nambala yake ya foni yomwe adandipatsa ndikutsika basi pasiteji ya kwathu ku Malaza ku Chintheche,” adafotokoza Drake.

Drake adamuimbira foni usiku omwewo kuti amve wayenda bwanji koma sadakambe zambiri.

Drake adati patadutsa masiku angapo, adamuyimbiranso kumpatsa moni, apa adali njoleyo idali itabwerera ku Dwangwa ndipo adayankhulitsana ngati ongodziwana chabe.

“Koma nditakhala masiku angapo, mtima wanga udayamba kukankha mwazi ndipo ndidamuyimbira kuti ndikadakonda titakumana bwino ndi kukambirana nkhani ina. Iye adati adalibe mpata chifukwa ntchito yawo amagwira sabata yonse, koma nditalimbikira adangoti ndidzapite nthawi ya nkhomaliro ndipo tidzakambirana kwa mphindi 30 zokha,”adatero Drake.

Ndipo tsikuli litakwana Drake adakampezadi Mada akadali kuntchito ndipo atakumana adamtengera kunyumba kwake komwe kudalinso anzake ena awiri. Apa adamkonzera chakudya ndipo adakambirana uku akudya.

“Adandifunsira banja, ndipo ndidamuuza kuti ndikaganize kaye,” adatero Mada.

Patatha masiku atatu, Drake adakokanso chingwe ndipo cimwemwe chidadzala tsaya Mada atanena kuti walola.

Abusa mayi Agness Nyirenda ndiwo adamangitsa ukwati ku Zolozolo CCAP mumzinda wa Mzuzu ndipo madyerero adali kusukulu ya sekondale ya Katoto.

Related Articles

Back to top button
Translate »