Chichewa

‘Mudali mu Sitandede 1’

Listen to this article

 

Dzina la Julius Mithi si lachilendo. Ndi kadaulo pa zowerengetsa komanso wagwirapo ntchito kubungwe la zamasewero la FAM. Ngakhale ambiri angamudziwe mkuluyu, zambiri za banja lake sizidziwika komanso momwe adatumbira namwali wake.

Mithi akuti naye ndi wosongoka pakamwa ndipo adatumba kale womusangalatsa. Uyu ndi Ella Msopa Kumwenda amene lero ndi mayi Mithi.

Mithi ndi mkazi wake Ella
Mithi ndi mkazi wake Ella

Ndi banja lachitsanzo, lonyadirana ndipo Mulungu sadalimane mphatso za ana awiri kuwonjezera chimwemwe chawo. Kodi nanga Mithi adamasuka bwanji pakamwa kuti athere mawu Ella?

Chithokozo chipite kwa makolo a awiriwa potumiza ana awo ku Vongo FP School m’boma Mzimba. Awiriwatu adaponyerana maso ali sitandede 1.

Kodi nthawi imeneyi Mithi adali atadziwa kale kusula Chichewa? “Ayi, timangokondana mwachibwana.”

Nanga Chichewa adasula pati? “Ndinachoka ku Vongo kubwera ku Mzuzu mu 1981 kudzakhala ndi bambo anga ndipo panadutsa zaka 7 pomwe sitinathe kuonana, kufikira ine nditayamba ntchito m’boma mu 1992. Apo Ella anali ku Ekwendeni Nursing School. Mwamwawi tinadzakumana ku Mzuzu pomwe chibwenzi chathu chidayambiranso. Atatha zaka 4 kusukulu ya unamwinoko tidakwatirana.”

Mithi akuti zinthu izi zidamukoka kuti asadumphitse mawu pa wokondedwa wakeyu: “Ndinamufunsira chifukwa adali mtsikana wofatsa komanso amachoka kwathu, kwawo ndi kwa agogo anga.”

Okondanawa akuti panthawiyo adalibe ndalama zomangitsira ukwati ndipo adangodalitsa ku St Peter’s Cathedral Parish ku Mzuzu mu 2008.

Mithi amachokera m’mudzi mwa Chandiwira Moyo, Senior Chief Mtwalo m’boma la Mzimba. Iye ndi woyamba kubadwa mwa ana anayi. Ella ndi wa m’mudzi mwa Mwelekete kwa Mtwalo komweko. Iye ndi woyamba mwa ana atatu ndipo amagwira ntchito zachipatala. Ponopa akupitiriza maphunziro a ukachenjede kuti azame kwambiri pantchito yake. n

Related Articles

Back to top button