Nkhani

Mudalinji m’chakachi?

Listen to this article
  • Ma alubino aona zakuda
  • Mpotopola ku Joni, Amalawi 3 200 athothedwa
  • Anthu 106 afa ndi madzi osefukira

 

Tili m’chaka china, 2015 wapita ndipo talowa 2016. Lero tikhale tikuunguza zina mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zidamera nthenje m’chaka changothachi.albinos

Maalubino aona mbonaona

Kwa nthawi yoyamba, dziko lino lidaona zomwe zakhala zikungomveka m’maiko ena. M’chaka cha 2015 taona maalubino akusakidwa ngati nyama. Kuwapha, kuwachotsa ziwalo, komanso kuwagulitsa kumene pokhulupirira kuti ziwalo zawo zingabweretse chuma.

Mchitidwewu udatenga malo ku Machinga, Balaka, Dedza komanso Mangochi. Nkhaniyi yakhala ikudandaulitsa bungwe lomenyera ufulu wa anthuwa la Association of People with Albinism in Malawi (Apam) malinga ndi mkulu wa bungweli, Boniface Massah.

Massah adati zonsezi zakhala zikuchitika chifukwa cha zilango zomwe mabwalo akhala akupereka kwa yemwe wapezeka wolakwa. Mwachitsanzo, m’boma la Dedza amayi ena adalamulidwa kukaseweza kundende zaka ziwiri atapezeka olakwa pankhani yofuna kusowetsa alubino, nkhani yomwe idadandaulitsa bungweli.

Mwezi wa March, anthu achialubino pamodzi ndi mabungwe adachita zionetsero mumzinda wa Blantyre pofuna kuonetsa mkwiyo wawo ndi zomwe zakhala zikuchitika.

Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalonjeza kuti athana ndi onse amene apezeke olakwa komabe ngakhale adalankhula motere, anthuwa akhalabe akukhala mobisala m’dziko lawo lomwe.

 

Madzi osefukira, anthu 106 afa pangozi za madzi

Pa 19 January chaka changothachi, ngozi idachitika m’maboma 15 m’dziko muno pamene madzi a mvula yosakata adasefukira ndipo maboma a Nsanje, Mulanje ndi Chikwawa ndiwo adakhudzidwa kwambiri, komanso maboma ena monga Rumphi ndi Karonga kumpoto.

Ngoziyi idachitika chifukwa cha mvula yomwe idagwa yochuluka m’dziko muno kwa sabata ziwiri osalekeza.

Anthu 145 000 adakhudzidwa m’maboma 6 ena adasamutsidwa m’malo mwawo ndi kukasungidwa m’misasa.

Anthu 106 adafa pangoziyi ndipo dera lokula ndi mahekitala 64 000 lidakokoloka. Kutsatira ngoziyi, matenda a kolera adabuka ndipo anthu 423 adakhudzidwa ndi matendawa omwe adapaha anthu 6.

Mutharika adalengeza kuti dziko lino ndi malo angozi ndipo kotero mabungwe ndi maiko akunja akuyenera kupulumutsa dzikoli kumavutowo. Mawuwa adachititsa kuti mabungwe akunja koma ena a m’dziko la Malawi momwemuno ayambe kupereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu amene adakhudzidwa.

 

Mtopola ku Joni, Amalawi athothedwa

Nkhani inanso yomwe idakula m’chakachi ndi zipolowe zomwe zidabuka m’dziko la South Africa kuchitira alendo amaiko ena amene akugwira ntchito m’dzikomo.

Maiko adayamba kusamutsa nzika zake m’dzikolo chimodzimodzinso dziko la Malawi mu April lidasamutsanso nzika zake 3 200 zomwe zidakhudzidwa ndi mtopolawo.

Mtopolawo udali wachiwiri dziko la South Africa likuchitira alendo amene akudzafuna maganyu m’dzikomo. Mu June 2008, dziko la South Africa lidachitiranso mtopola alendo a m’maiko ena amene akukhala m’dzikolo ndipo anthu 60 adaphedwa pamene anthu oposa 600 adavulazidwa.

Lero pamene mwachita bata m’dzikomo, Amalawi ambiri akhamukiranso m’dzikomo kukafuna maganyu.

Ziwawazo zidayamba pamene mfumu ya Mazulu Gooodwill Zwelethini idakolezera moto ponena kuti nzika za m’maiko ena zibwerere kwawo ati chifukwa zikuwaphangira ntchito.

Ngakhale utsi sufuka popanda moto, Zwelethini adakana izi ponena kuti atolankhani ndiwo sadamumvetse.

Maiko komanso mabungwe mu Africa adadzudzula zomwe zochitika m’dzikolo.

Dziko la Nigeria nalo lidayamba kusala nzika za dziko la South Africa. Ku Zimbabwe, mawailesi a m’dzikolo adayamba asiya kuimba nyimbo za m’dziko la South Africa, pamene ku Mozambique, nzika zina za m’dziko la South Africa zidachitidwa chipongwe.

Ku Malawi kuno anthu adachita zionetsero pamene adakapereka chikalata cha madandaulo awo kwa kazembe wa dziko la South Africa. Kuphatikiza apo, Amalawi adachitanso zionetsero zina zokakamiza kuti anthu asamagule katundu m’sitolo za m’dziko la South Africa zimene zili m’dziko muno monga Shoprite, Game ndi Pep.

 

Boma lichotsa mafumu am’tauni

Nkhani ina yomwe idazunguza m’chakachi mpaka lero ndi ya ganizo la boma lofuna kuchotsa mafumu m’mizinda, m’tauni komanso m’mamanisipalite.

Unduna wa maboma ang’ono ndiwo udatulutsa chkalata chomwe chidadzetsa kusagwirizana pamene mafumuwo adaopseza boma kuti achita zomwe angathe pofuna kuteteza ufumu wawo.

chikalatacho mwa zina, chidati mafumuwo sazilandiranso mswahara chifukwa tsopano ndi anthu wamba. Gawo 3 (5) la malamulo okhudza ufumu (Chiefs Act) ndi lomwe lidaomba mkota paganizo la bomalo.

Mafumu a mizinda ya Lilongwe, Mzuzu, Zomba ndi Blantyre komanso manisipalite za Luchenza ndi Kasungu, ndiwo adakhudzidwa ndi chikalatacho.

Nkhaniyi itafika pampondachimera, boma lidabweza moto  ndipo mafumuwa akugwirabe ntchito yawo monga kale.

Boma liletsa masacheti

M’chaka chimenechi dziko la Malawi lidabwera ndi ganizo loletsa mowa wa m’masacheti.

Msonkhano wa nduna za boma udavomereza zoletsa mowawu ndipo kwangotsala kuti pakhale lamulo lokakamiza aliyense kusiya kugulitsa mowawu.

Related Articles

Back to top button
Translate »