Chichewa

Muli mafunso m’manifesito a DPP

Listen to this article

Chipani cha DPP chatulutsa manifesito ake Lamulungu pa 7 April amene akufotokoza zomwe chipanichi chakwaniritsa m’zaka zisanu zathazi komanso zomwe chipange ngati chisankhidwenso pa May 21.

Zambiri zomwe DPP yasanja ndi zomwenso chidalonjeza pokonzekera chisankho cha 2014.

Chipanicho chasiya mfundo zina zomwe sichidakwaniritse mu 2014 monga kuchepetsa mphamvu za mtsogoleri wa dziko, kukozanso doko la Nsanje mwazina.

Manifesito a DPP akubwera pamene chipani cha MCP ndi UTM atulutsa kale mfundo zomwe achite ngati atasankhidwa.

DPP yati akangochipatsanso zaka zina zisanu, chithetseratu katangale m’dziko muno ntchito yomwe ati adayamba kale kuigwira mu 2014.

Pothandizira mfundoyo, DPP yati idzamanga komanso kuchotsa pa ntchito aliyense amene adzapezeke akuchita ziphuphu.

Yatinso idzakhazikitsa khoti lapadera lothana ndi milandu ya katangale mfundo yomwe ilinso m’manifesito a MCP.

Chipanicho chati chikapatsidwa zaka zina zisanu chidzatsitsa mtengo wa feteleza dziko lonse komanso ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo yomwe ilipo pano idzakhalapobe.

Chatinso anthu amene alibe malo wolimapo, boma lidzawapatsa ndalama zomwe aliyense adzasankha chomwe adzachite nazo.

Chipanicho chalonjezanso kuti ntchito yomalinga nyumba zamakono kwa osauka ndi achikulire idzapitirira.

Chipanicho chatinso chidzaonetsetsa kuti Amalawi ndiwo akupanga bizinesi m’midzi osati anthu obwera.

Anthu akunja akuti azizapanga mabizinesi m’matauni mokha ndi m’mizinda ndi mpamba wa pafupifupi US$250 000 (K185 miliyoni) womwe adzabwere nawo kuchokera kunja. Ndipo bizinesi yosaposera K50 miliyoni idzapatsidwa kwa Amalawi okha kuti apange.

Chipanichi chatinso chidzaonetsetsa kuti dotolo mmodzi akuthandiza anthu 5 000 osati 33 000 monga zilili pano ndipo akuti izi zichitika m’zaka zisanu zikudzazi.

M’sukulu zonse za ukachenjede akuti ophunzira azizagwiritsira ntchito intaneti yaulere.

Mwa zina, manifesto a DPP ati m’zaka zisanu zikubwerazo, chipanicho chidzapereka ndalama zokwana $3.5 biliyoni (K2.5 thililiyoni) zotukulira ntchito za mtengatenga, mphamvu za magetsi, ulimi wa mthilira, maphunziro, umoyo, zokopa alendo komanso zotumizirana mauthenga mwa njira za makono zomwe zidzapititse patsogolo chuma cha dziko lino.

Chipani cha DPP chati chidzaika pafupifupi K2.7 thililiyoni yomangira zinthu zosiyanasiyana m’dziko muno kuchokera chaka cha 2019 mpaka 2024.

DPP ikuti idzamanga msewu wamakono kuchokera ku Mzuzu kudutsa Lilongwe mpaka kufika ku Blantyre.

Chipanicho chatinso chidzagula madesiki kwa ophunzira onse m’sukulu zonse m’dziko muno.

Koma akadaulo pa ndale ati manifesito a chipani cha DPP avuta kuwakhulupirira chifukwa zambiri zomwe akukamba ndi zomwe adalonjezanso mu 2014 ndipo chalephera kukwaniritsa.

George Phiri wa ku sukulu ya Livingstonia komanso mneneri wa Malawi Political Science Association, Andrew Mpesi ati anthu sangawerenge manifesito a DPP ndi diso limodzi lokha koma kuunikiranso zomwe akwaniritsa m’zaka zisanu zapitazo.

“Chitsanzo, mu 2014 adalonjeza kuti adzathana ndi ziphuphu, zaka zisanu zatha koma pafupifupi tsiku lililonse nyuzipepala zikuvumbulutsa katangale amene akuchitika m’bomamu. Panonso akukamba zothetseratu ziphuphu ndiye mbali iyi zivuta kukhulupirira kwake,” adatero Mpesi.

“Vuto la manifesito a chipani cholamula mkuti anthu amayang’ana kaye zomwe achita ndi zomwe akulonjeza,” adaonjeza.

Kuona kwa Phiri adati manifesito amene DPP yaphika pano sakusiyana ndi omwe idatulutsa m’chaka cha 2014.

Iye adati zambiri zomwe alukamo ndi zomwe alephera kukwaniritsa kuyambira mu 2014.

“Panopa zivuta kuwakhulupirira, kodi chinthu achilephera kukwaniritsa m’zaka zisanu panopa ndiye akwanitse kuchikwaniritsa?” adadabwa Phiri.

Iye adati DPP idataya mwayi kukachita nawo mtsutso chifukwa ndi womwe ukadawapatsa danga kufotokozera bwino pamene padavuta kuti akwaniritse masomphenya awo ndi momwe akwaniritsire ulendo uno.

Phiri akuganizanso kuti palibe chisinthe ngati DPP ingapambane pachisankho cha pa May 21 chifukwa manifesito awo sakunena momwe adzakwaniritsire zomwe adazilephera.

“Ndikuona ngati manifesito a UTM ndiwo akufotokoza bwino motsatirana ndi MCP chifukwa nkhani zomwe asanja ndi zomwe anthu akukumana nazo komanso akufotokoza bwino momwe adzakwaniritsire.

Mu 2014, DPP idalonjeza kuti pofika 2019 sipadzapezeka mwana akuyenda mtunda woposera makilomita kupita kusukulu zomwe sizidatheke.

Chidatinso chidzapereka chitetezo kwa munthu aliyense, koma kuchokera 2014, anthu 25 achialubino aphedwa, 11 akusowa ndipo nkhani zokhudza anthuwa zafika pa 153.

Chipanichi chidatinso m’zaka zisanu chidzamanga nyumba 10 000 za apolisi koma izi sizidatheke.

Related Articles

Back to top button