Chichewa

Mulibe Sisters ali kuti?

Listen to this article

Tikamalira, muzitimvera

Tikamalira, musamakwiye

Mudziwe ndife ana anu

Sindikudziwa kuti nyimbo ya Lucius Banda idabwera bwanji m’mutu mwanga. Ndipo sindikudziwa chifukwa chimene nyimboyo idayalira mphasa m’mutu mwangamo.

Mwinatu malingaliro adali pazochitika mu 2012 pomwe nyimbo ya Achoke! Achoke! idali pakamwa pamavenda ambiri. Nthawiyo nkuti anyamata ena otchedwa Paki atauza Mfumu Mose kuti apakire zake pasanathe miyezi iwiri. Miyezi iwiri isanati kutha, Mfumu Mose nkuti itapita kumadzi kukazula chinangwa. Ndipo inali isanatiuze ngati anyamata aja apachibale Mustafa ndi Ajibu angalandirane mpando wonona pano pa Wenela.

Anyamatatu a Paki si pano. Ndikumbuka adamufumbatitsa mpweya gogo uja adandipeza nditavula shati pomwe ndinkalima kwathu kwa Kanduku ndipo adalowera uku ndi uko kunena kuti adatipeza tili chinochino.

Abale anzanga, Paki si pano! Paki palibenso.

“Koma kodi amvanako kuti chiyani? Kodi anenapo chiyani pazakupezeka kwa chakudya? Tileka liti kugona m’misika ya Admarc?” adafunsa Abiti Patuma.

Bambo amene adali naye adamudula.

“Akuluakulu, inetu ndili m’madzi. Dzulo ndinatenga msungwana wina m’galimoto yanga. Sindimamudziwa koma panjira adakomoka. Ndidapita naye kuchipatala. Atakhala nthawi pang’ono dotolo adati wasangalala kuti mkazi wangayo wabala mwana.

“Ndidamuuza dotoloyo kuti si mkazi wanga. Koma atamufunsa mkaziyo, adanenetsa kuti ndine mwamuna wake. Ndidati tiyezetse ngati mwanayo adalidi wanga. Atandiyeza dotolo adati sizingatheke kuti ndikhale bambo chifukwa ndidagwa mumtengo wapapaya. Chomwe chidandiliza nchakuti mkazi wanga ali ndi ana anayi. Tsono bambo wa anawo ngati si ine ndi ndani?” adamaliza mkuluyo.

Ndidafuna kuseka. Ndidafunanso kulira nthawi yomweyo.

Tidaona anthu akulimbana pa Wenela. Tidakhamukira kumeneko. Tidaona kamnyamata kena kakugawa chimanga. Onse ankangoti Major! Ine amvekere Go higher man of God! Mnyamatayo adali kugawa chimanga.

“Ndithu this is miracle maize. Mukakagayitsa chimangachi, ndithu dengu lanu silidzatsikanso. Miracle maize! Zikuonekatu zija adaona mayi uja adasunga Elisha masiku adzana,” adatero mnyamata uja.

Inetu paja zoweruza ayi.

Mkazi wa mnyamata uja, Meliya, adaima: “Ndikuchitira umboni ine. Mayi wina adabzala mbuto kumpingo wathu wounikirawu. Adapita kubanki kukatenga ngongole imene adagulira galimoto. Koma kuti ayambe kubweza ngongole, abanki adati mapepala ake asowa. Go higher! Shout a better Amen!”

Ndiyo nkhani tidabwerera nayo pa Wenela.

“Kodi Moya Pete amene akuoneka kuti zikumulakayu sakadamupeza mnyamatayu kuti chimangachi akuchipeza kuti? Ndithu akadakapezako mmalo momangonena kuti chiliko kumsika.

“Sangayerekeze,” adatero Abiti Patuma. “Akadakhala wanzeru akadapita kukagwada kwa Mulibe Sisters kunena kuti amukhululukire. Mwaiwala kale kuti Mfumu Moya isanapite kumtsinje kukazula chinangwa ndipo njala idasautsa pano pa Wenela, tidapulumukira chimanga cha Mulibe Sisters amene adachibweretsa pano pa Wenela, ku Ndirande, Chirimba, Chilomoni, Bangwe, Ndirande ndi madera ena?” adatero Abiti Patuma.

Palibe icho ndidatolapo.

Gwira bango mwa iweeeee! Upita ndi madzi! n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »