Chichewa

Musasusukire dzombe—unduna

Listen to this article

 

Ngakhale dzombe limaononga mbewu, kwa anthu ena ndi ndiwo zankhuli. Koma unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi wachenjeza kuti anthu asasusukire dzombe lomwe lapoperedwa mankhwala.

Dzombe lidagwa ndi kusakaza mmera wamthirira ndi nzimbe m’madera a chigwa cha Shire, nkhani yomwe yadula chiyembekezo cha mpumulo pankhani ya njala.

Mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga, Lachitatu adati ngakhale mankhwala omwe akupoperedwawo sapha dzombe, akhoza kukhala ndi zotsatira zoipa pamoyo wa munthu.

Koma Lachinayi nyuzi ya Nation idayankhula ndi mneneri wa kampani yopanga shunga ya Illovo ku Ntchalo m’boma la Chikwawa, Irene Phalula, yemwe adatsimikiza zoti kampaniyo idapopera mankhwala a fipronil omwe adapha dzombe miyandamiyanda patatha maola 24 chipopereni.

Maganga: Musadye dzombe lopopera
Maganga: Musadye dzombe lopopera

Mosakaika anthu ena poona dzombe lakufalo amangoti laponda lamphawi, ndiwo zapezeka, osadziwa kuti akuika miyoyo yawo pachiposezo.

“Vuto ndi lakuti anthu ambiri amakonda zinthu zobwera mosavuta pomwe ena amaona ngati apeza mpamba wa bizinesi ndiye, ngati unduna, tikunenetsa kuti dzombeli si labwino kudya, ayi,” adatero Maganga.

Iye adati zomwe achita a kampani ya Illovo n’zotamandika chifukwa kulilekerera, dzombe likadakhoza kufalikira m’madera ambiri ndi kuononga mbewu ndi zomera zina.

Mfumu yaikulu Malemia ya ku Nsanje yati n’kofunika kumva malangizo a akatswiri monga a kuunduna wa zamalimidwe kuti anthu asaononge miyoyo yawo kapena ya anthu ena.

Dzombe ndi mtundu wa ziwala zomwe zimayenda m’chigulu ndipo likangofika pamalo limaononga zomera moti kulilekerera likhoza kukhala gwelo la njala ndi umphawi waukulu m’dziko muno.

Dzombeli lidaoneka sabata yatha ku Bangula m’boma la Nsanje komwe lidayambira utumiki wake wosakaza mbewu, makamaka chimanga chamthirira m’mahekitala 30.

Sabata ino, dzombeli lidafika m’boma la Chikwawa komwe mkulu wa zamalimidwe, Ringston Taibu, komanso mneneri wa kampani yopanga shuga ya Illovo ati laononga mahekitala 405 a nzimbe.

Phalula adati kampani ya Illovo ili kalikiriki kupopera mankhwala m’minda ya nzimbe koma adati mankhwalawo sapha dzombe koma kungolifoola kuti lisiye kuwonongako.

“Dzombeli lidafika usiku wa Lolemba ndipo lidagwira munda wa mahekitala 50 a nzimbe lisadalowerere m’munda wina wa mahekitala 120. Kuchoka apo lidakagwiranso munda wina wa mahekitala 115 kufupi ndi munda womwe tikuchitira ulimi wamthirira,” adatero Phalula.

Iye adati usiku womwewo kampani itaona kuti dzombelo likhoza kulowerera kumunda wamthirirawo, idayamba kupopera mankhwala koma adati kuwonongeka kwa nzimbeko sikusokoneza makololedwe.

Taibu adati mankhwala a cypermethein, omwe kampaniyi idapopera poyamba, amangofowola dzombe osati kupha ngati momwe mankhwala a fenetrothion ndi fipronil amachitira. n

Related Articles

Back to top button
Translate »