Nkhani

Mutharika asosola nthenga atsogoleri

Listen to this article

….asankha nduna, koma Chimunthu Banda aukana

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika sabata imene ikuthayi anali wotangwanika zedi chifukwa ndiye wasosola nthenga akuluakulu ena m’boma ngakhalenso m’chipani chake cha Democratic Progressive Party (DPP).

Chimunthu Banda (Kumanja) wakana unduna wa zamigodi

Lachinayi, Mutharika adasankha nduna zatsopano 32 kuphatikizapo zochokera kuchipani cha United Democratic Front (UDF) chomwe ali nacho mumgwirizano komanso Henry Chimunthu Banda, yemwe adapikisanapo ndi Mutharika pofuna kuimira DPP mu 2014. Dzulo Chimunthu Banda adakana undunawo.

Koma Mutharika, polengeza ndunazo, sanatchule dzina la wachiwiri wake Saulos Chilima, yemwe bwalo la Constitutional Court  lidati abwerere pampando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko. Gawo 79 la malamulo a dziko lino limaneneratu kuti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino amayenera kukhala m’gulu la nduna za boma.

Ndipo Mutharika adasankha Atupele Muluzi, Lilian Patel komanso Clement Chiwaya kuchokera kuchipani cha UDF pamndandanda wa ndunazo.

Zina mwa nduna zimene zabwerera ndi Everton Chimulirenji, Chipiliro Mpinganjira, Bright Msaka, Ben Phiri, Joseph Mwanamvekha, Ralph Jooma, Mary Navicha, Jappie Mhango, Nicholas Dausi,  Symon Vuwa Kaunda, Salim Bagus ndi Mark Botomani.

Ena mwa amene angosankhidwa kumene ndi Kamlepo Kalua, Kenneth Ndovie, Grace Kwelepeta, Chimwemwe Chipungu, Grezelder Jeffrey komanso Mary Makungwa.

Pambali pa izi, Mutharika adasonyezanso mphamvu zake  m’sabatayi pomwe adakana mabilo ofuna kusintha malamulo a zisankho komanso adakana kumva pempho la komiti yoona zolemba ntchito akuluakulu ena m’boma la Public Appointments Committee (PAC) kuti iye achotse makomishona a bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Iye adakananso kusayinira mabilo ofuna kusintha malamulo ena oyendetsera zisankho popeza adati akutsutsana ndi malamulo aakulu a dziko lino.

Pambali pochotsa nduna zake zonse sabata yatha, Mutharika m’sabatayi adachotsa mkulu wa asilikali Vincent Nundwe ndi wachiwiri wake Clement Namangale ndi kusankha Andrew Namathanga kukhala mkulu wa asilikali komanso Davis Mtachi kukhala wachiwiri wake. Iye adasinthanso mipando ya akuluakulu ena a asilikaliwo.

Kusinthako kudafikanso kuchipani chake cha Democratic Progressive Party (DPP) komwe Mutharika adachotsa magavanala a kumpoto (Ken Sanga) ndi pakati (Bintony Kuntsaira). Iye adasanha Christopher Mzomera Ngwira kukhala gavanala wa kumpoto komanso David Kambalame kukhala gavanala wa pakati.

Nako kupolisi mipando ya akuluakulu ena idasintha pomwe akuluakulu ena m’zigawo adasamutsidwa mosiyanasiyana.

Malinga ndi kadaulo wa zandale ku Chancellor College Mustapha Hussein adati kusasainako kuonetsa kuti Mutharika akufuna anthu adziwe kuti ndiye ali pa chiongolero.

“Akufuna kuonetsa kuti akulamula ndiye ngakhale pali chikonzero choti chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chichitikenso,” adatero Hussein.

Lachiwiri, Mutharika kupyolera mwa mneneri wake Mgeme Kalilani adati sangachotse makomishona monga a PAC adapemphera chifukwa padali zokhota zina.

“Ndidalandira lipoti la PAC ndipo ndaliwerenga koma lili ndi zofooka zambiri. Mwa zina, silikunena ngati makomishona adauzidwa za zofooka zawo asadakaonekere, ngati adapatsidwa mpata wolumikizana ndi maloya awo komanso likuoneka ngati adangotengera chigamulo cha khoti chomwe tidapanga apilo kukhoti lalikulu la Supreme,” adatero Mutharika.

Iye adapitiriza kuti makomishona omwewo ndiwo adayendetsa chisankho cha aphungu ndi makhansala zomwe zidavomerezedwa ndiye zidatheka bwanji kuti asakhale akadaulo pachisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chokha.

“Pa zifukwa izi, apulezidenti akuti sadavomere lipoti la PAC ndipo sachotsa komishona aliyense kuphatikizapo wapampando wake Jane Ansah mpaka chigamulo cha apilo,” adatero Kalilani.

Bwalo lounikira malamulo aakulu kwambiri m’dziko lino lidagamula pa 3 February 2020 kuti komitiyo iunike makomishona onse mmodzimmodzi ngati ali oyenera kuyendetsa bungwe la MEC ndipo lipereke zomwe lipeze kwa mtsogoleri wa dziko lino.

Chigamulocho chimatsatira samani ya mtsogoleri wa Malawi Congress Party (MCP) Lazaru Chakwera ndi wa UTM Party Saulos Chilima omwe adadandaula kuti bungwe la MEC ndi chipani cha DPP adasokoneza chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino cha pa 21 May 2020.

Related Articles

Back to top button
Translate »