Sukulu ya zaudotolo ya College of Medicine (COM) yasintha momwe mwambo wa maliro panyumba ya chisoni ya pasukuluyo mumzinda wa Blantyre uzichitikira kuyambira pa November 1 2015.
Tsopano, galimoto imodzi yokha ndiyo iziloledwa kufika kumalowa yomwe izikhala ndi anthu osaposera 10. Panja pampanda wa sukuluyu pamene galimoto zimaima, tsopano sipakuloledwanso kuti paime galimoto.
Woyendetsa sukuluyu Margaret Longwe adatsimikizira Msangulutso Lachinayi m’sabatayi ndipo adati anthu asaope ndi kusinthaku.
Nayo mitengo yosamalira mtembo yasintha. Kuumitsa thupi (embalming) tsopano ndi K50 000 kuchoka pa K10 000, kusunga usiku umodzi ndi K10 000 kuchoka pa K1 000 pamene kusambitsa ndi kuveka ndi K15 000 kuchoka pa K10 000.
China chomwe chasintha nkuti kumaloku sikuzikhalanso mwambo oona nkhope kapena mwambo wa mapemphero ndipo mmalo mwake izi zizikachitika kunyumba kapena kumpingo.
Koma Longwe akuti zonsezi zachitika kufuna kusamala malowa. “Palibe chodandaulitsa apa, dziwani kuti iyi ndi sukulu. Kukachitika maliro, kumabwera anthu ambiri mpaka kumachitira mapemphero zomwe si zabwino polingalira kuti apa ndi pasukulu.
“Panjapanso pamakhala galimoto zambiri moti ndi mwayi bwezi tikukamba kuti pachitika ngozi koma sizidachitikepo. Ndiye zonsezi tachita kuti tithandizane ndi anthu omwe amagwiritsira malo ano,” adatero Longwe.
Iye adati anthu akapita ndi thupi kumaloko, azifunsidwa kaye ngati akwanitse kutsatira malamulo atsopanaowo ndipo akakana, thupilo lizibwezedwa.
Atafunsidwa kuti alankhulepo pa za kukwera mtengo, Longwe adati iyi si nkhani yoti tikambirane.
“Sitikulengeza mitengo m’nyuzi, ndipo simudamvepo tikulengeza. Aliyense amadzamva komwe kuno akabwera za mitengo. Palibe nkhani pamenepa koma kungowadziwitsa anthu kuti iiyamba ndondomeko zatsopanozi pa 1 November,” adatero iye.
Wophwanya lamuliro, akuti adzalipa K50 000.