Nkhani

Mwambo wa ufumu pakati pa Achewa

Listen to this article

Ufumu ndi udindo wa utsogoleri womwe umalira munthu waluntha ndi wakhama komanso wachikondi ndi wachilungamo kuti mudzi mtundu usasokonekere komanso pakhale chilungamo ndi mtendere. Wapampando wa gulu la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo) Professor George Kanyama Phiri akufotokozera STEVEN PEMBAMOYO momwe mwambo wa ufumu umayendera pakati pa Achewa.

Kanyama: Amayi amatenga gawo lalikulu
Kanyama: Amayi amatenga gawo lalikulu

Ndikudziweni.

Ndine Professor George Kanyama Phiri ndipo ndine wapampando wa gulu la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo) muno mmalawi udindo omwe ndidaulandila kuchoka kwa a Justin Malewezi.

Poyamba tandiuzani za utsogoleriwu kuti umayenda bwanji.

Utsogoleri wa gulu limeneli umasiyana ndi utsogoeri wa magulu kapena mabungwe ena chifukwa siutengera chisankho ayi koma mwini wake mfumu ya Achewa Kalonga Gawa Undi amachita kusankha akaona kuti wina watsogolerapo ndipo wakhutira naye.

Chabwino nkhani ili pano ndi ufumu pakati pa

Achewa. Kodi ufufmuwo umayenda bwanji?

Ufumu wa Achewa umayendera kwa amayi kusiyana ndi mitundu ina yomwe imatengera abambo. Mfumu ikakalamba kapena kumwalira, amaona kuti kodi kumakolo ake kuchokera kwa azimayi angavale ufumuwo ndani. Amayambira ku banja lalikulu nkumatsika mpaka atapezeka olowa ufumuwo.

Amasankha ndani ndipo amasankha bwanji?

Amasankha ndi amayi a kubanja la chifumulo. Mfumu ikakalamba, amayi amakhala pansi nkuunika kuti angadzalowe mmalo ndani ndipo akapezeka amauza madoda (abambo) omwe amaitanitsa mlowammaloyo nkupanga zoti aziyenda ndi mfumuyo kulikonse kuti aziphunzirako zina ndi zina. Chimodzimodzi mfumu ikamwalira, msangamsanga azimayi amakhala pansi nkusankha mlowammalo.

Nanga bwanji pamapezeka kuti ena akulimbirana ufumu mpakana kubwalo lamilandu?

Pamwambo wa Chichewa kumene kuja nkulakwitsa chifukwa ndondomeko ilipo kale ndipo ndiyokhazikika yongoyenera kutsatidwa. Mpata woyamba kubanja la amayi aakulu kenako owatsatira kukamalizira kumunsi mpaka mlowammalo atapezeka. Zimatheka kuti amayi akuluakulu onse osasankhako mfumu chifukwa pali zomwe azimayiwo amaona posankha.

Zinthu monga ziti?

Zilipo zambiri monga khalidwe la munthu, chilungamo, maonekedwe chifukwa mfumu imafunika izikhala yolemekezeka mmaso kuti ikalankhula kapena kugamula mlandu anthu aziti apa pagamulidwa mlandu osati kumaderera. Mfumu amafunikanso kukhala wachilungamo, opanda ziphuphu, odziwa kugawa, wachikondi ndiwolimbika pochita zinthu kuti anthu ake azimutsatira.

Ndiye akasankha dzinalo chimachitika nchiyani?

Amayi akasankha dzina la mfumu, amakapereka dzinalo kwa abambo omwe amapitiriza zina zonse monga kutumiza mauthenga kwa mafumu ena komanso kuofesi ya DC ndi kukonza tsiku la mwambo oveka ufumu. Muyenera kudziwa kuti ufumu wa Chichewa amaveka ndi mafumu akwina osati eni ake ayi ndiye mafumu oterowo amayenera kulandira uthenga nthawi yabwino.

Ntchito ina ya amayi ndi chiyani pamwambo wolonga mfumu?

Mwachidziwikile azimayi ndiwo amakonza zakudya ndi zakumwa pamwambo koma kupatula apo, amakhalanso ndi ntchito yokonza anamwali chifukwa pamwambo wa ufumu, Achewa amatengerapo mpata wolanga anamwali. Uwu uli ngati ulemu wapadera wa mafumu komanso amayi amathandiza kwambiri kumbali ya magule okometsela mwambo.

Nanga pamwambopo pamakhala zotani?

Pamwambo wa ufumu wa Achewa pamakhala magule amakolo, pamakhalanso kufotokoza mbiri ya ufumu omwe ukuvekedwawo kenako bwanamkubwa amawerenga malamulo a kayendetsedwe ka ufumu nkuveka olowa ufumuwo mkanjo wa ufumu kwinako magule ndi madyelero amapitirira.

Pali china chomwe chimachitika ufumuwo ukavekedwa?

Kwambiri kwake. Mafumu amakonza tsiku lotengera mfumu yatsopanoyo kulikulu ku Mkaika kukayionetsa kwa Kalonga Gawa Undi. Kumeneko amakamulandira ku Mphasa. Mphasa ndi malo omwe mafumu okhaokha amakumanirako pakakhala zokambirana kapena akamakonza mwambo wina ulionse. Ndi malo olemekezeka kwambiri. n

Related Articles

Back to top button
Translate »