Nkhani

Mwambo woika maliro a khanda lozizira

Listen to this article

Amalawi ngakhale ali ndi miyambo yosiyanasiyana malinga ndi mitundu yawo monga Achewa, Angoni, Atumbuka, Alhomwe, Amang’anga, Asena kaya ndi Ayao, koma pamwambo woika khanda lopitirira zochitika zimakhala zofanana. DAILES BANDA adacheza ndi mayi Catherine Ligowe kuti afotokoze mmene mwambo woika khanda lozizira umayendera. Adacheza motere:Grave_commonwealth

Ndikudziweni mayi wanga.

Ndine Catherine Ligowe. Ndidabadwa zaka zambiri zapitazo. Ndimachokera ku Ntcheu m’mudzi mwa Chikadya, T/A Ganya. Ndili ndi ana asanu ndi awiri. Ndinenso namkungwi kumudzi kwathu komanso ndidali mzamba.

 

Kuno ku Mzuzu mukupezekako bwanji?

Mavuto mwanawe. Kuyeseyesa kuti tipezeko koponyako mkamwamu.

 

Ku Mzuzu kunonso ndinu namkungwi?

Ayi, ku Mzuzu kuno unamkungwi wanga umakhala wa m’makwalalamu koma kumudzi ndi komwe ndimagwira ntchitoyi kuchinamwali, tere chaka chomwechi ndidali komweko.

 

Mutiuzeko pang’ono za maliro akhanda lopitirira

Inu mufuna mudziwe chani?

Tiyambe ndi mwambo wa maliro mmene umakhalira.

Khanda lopitirira limatchedwa kuti khanda lozizira chifukwa mayi a khanda lija amakhala kuti sadakhale kaye pamodzi ndi mwamuna.

 

Mukutanthauza kuti khanda litamwalira pamiyezi iwiri makolo ake asadakhalire malo amodzi mwambo wake umakhala ngati wa khanda lopitilira?

Eya, chifukwa timakhulupirira kuti mwanayo sadatenthetsedwe ndi bambo ake.

 

Zimayenda bwanji?

Mwana uja akamwalira amakaikidwa ndi azimayi okhaokha koma azimayi aja saloledwa kulira malirowo chifukwa kulira kuja kumachititsa kuti mayi uja asadzaberekenso. Manda a malirowa sakhala akuya ngati a maliro a munthu wamkulu.

Chifukwa chiyani sakhala akuya?

Kalekalelo makolo athu ankakhulupirira kuti manda a khanda lozizira akakhala akuya kwambiri mayi wa khandalo sadzaberekanso.

Ndiye maliro a mapasa mumachita bwanji?

Akamwalira mmodzi mwa ana amapasa azimayi akalira malirowa timakhulupirira kuti mwana wotsala uja amamwaliranso, komanso tikamaika malirowa timaika khanda lomwaliralo ndi mvunguti pambali pake kuti mzimu wake uziona ngati akadali ndi mnzake uja.

Nanga wotsalayo mumatani naye?

Ameneyo timamusambitsa mumankhwala kuti mzimu wa mnzake uja usamamubwerere.

 

Tsopano inu mumati mudali mzamba, mudabadwitsako mwana wopitirira?

Ayi, palibe mwana wopitirira amene ndidabadwitsako.

 

Mudasiyiranji ntchitoyi?

Boma lidaletsa komanso anthu amene amabereketsa azimayi amafa maso n’chifukwa chake anamwino ambiri ochiritsa azimayi kuchipatala amakhala ovala magalasi. Kalekalelo mzamba asadayambe kugwira ntchito amayamba kaye wasamba mankhwala kuti adziteteze ku ukhungu.

 

Chimachititsa kufa masoko ndi chiyani?

Chimachitika ndi chakuti azimayi akamabereka amachita zinthu zodabwitsa zambiri ndiye ukaona zinthu zimenezo kwanthawi yaitali maso aja amafa, umangoona zinthu mwa mbuu.

 

Zikomo kwambiri chifukwa cha nthawi yanu.

Zikomo.

Related Articles

Back to top button
Translate »