Nkhani

Mwambo ‘wopha mudzi’ poika mfumu

Listen to this article

Anthu ena amakhulupirira kuti akamwalira amayenera akaikidwe chatsonga kapena kuti chokhala. Izi zimachitika kwambiri pakati pa mafumu Achingoni maka a kwa Maseko. Umu ndi momwe zidakhalira ndi maliro a T/A Bvumbwe wa ku Thyolo mwezi wathawu, yemwe adaikidwa chatsonga. Anthu otere akamwalira, pamakhala mwambo wopha mudzi. Izi zimachitika pokumba nyumba yoti igone mfumuyo. BOBBY KABANGO akutsata momwe zimakhalira.

Pepani wawa ndi zovutazi. Koma ndimati tichezepo pang’ono za miyambo ina yokhudza maikidwe a mfumu Yachingoni. Koma poyamba tidziwane.Ngoni_elder_with_inkosi_gomani

Ndine Opesi Mangombo ndipo kwathu ndi mom’muno mwa Bvumbwe.

 

Ndinu wa mtundu wanji?

Mukadzaona nsalu ya Gomani chonchi komanso mthini pamutu, musadzafunse, dziwani kuti amenewo ndi Angoni ankhondo aja amene adachoka ku Mozambique ku Domwe. Moti ine ndi Mngoni, ndili kumtundu wa Bvumbwe.

 

Ndamva kuti inu ndiye mumatsogolera adzukulu okumba manda a mfumu…

Mwamva zoona koma si kuti ndi manda onse, koma kuti ndinatsogolera adzukulu amene akumba manda amene tiike thupi la mfumu yathu Bvumbwe.

 

Timamva za mawu oti ‘kupha mudzi’ pamene mukukumba manda ogona mfumu, zimatanthauzanji?

Choyamba dziwani kaye kuti mfumu yathu igona chatsonga, kupha mudzi kumachitika ngati mukukumba manda a munthu amene akaikidwe chatsonga. Kwa iwo okaikidwa chogona ndiye sikukhalanso kupha mudzi. Mudzi ndi malo kapena kuti phanga lomwe mfumuyo imaikidwako. Choyamba mumakumba dzenje lotalika ndi mamita atatu ndi theka. Limakhala dzenje lozungulira, osati lamakona anayi monga zikhalira ndi ena. Mukamaliza kukumbako ndiye mumakhala pansi kupanga mudziwo.

 

Fotokozaninso, mwati mudzi n’chiyani?

Mudzi ndi malo kapena kuti phanga lomwe mfumu igoneko. Pamene mwakumba ndi kumaliza manda, ndiye mumayamba kupanga phanga. Kukula kwake kufanane ndi kukula kwa bokosilo. Koma nthawi zambiri mudziwo umakula ndi mamita awiri m’litali ndi m’lifupi.

 

Ndiye mukati ‘kupha mudzi’ mumatanthauza chiyani?

Timatanthauza ntchito yomwe mumachita kuti muyambe kupanga phangalo lomwe kulowe mfumu yathu.

 

Zimatheka bwanji kuti mupange phanga loti muli kale m’dzenje?

Timaonetsetsa kuti dzenjelo likhale lokula bwino kuti mukathe kukhala pansi ndi kumagoba mudziwo. Timapangira khasu lomweli koma timaligulula ndi kulizika ngati nkhwangwa.

 

Mukamaliza mumatani?

Tikafikira mlingo womwe tikufuna, timatenga timitengo ndi kukhoma pakhomo pa mudziwo chifukwa bokosi likalowa, timayenera titseke pakhomopa kuti dothi lisalowe. Simungapange mudzi musadayeze kukula kwa bokosi lomwe mfumu yathu igonemo.

 

Dothi lakenso liti?

Pajatu dzenjeli timalikwirira pamene taika mfumu yathu, ndiye pakhomo pa mudzi timatsekapo kuti dothi lisamupeze.

 

Koma cholinga chopangira mudziwu n’chiyani?

Mfumu siyenera kuthiridwa dothi pamutu. Mudziwu umapangidwa dala kuti ipeze kobisala pamene tikuthira dothi.

 

Ndi manda ngati awa, chiliza chake chimakhala chotani?

Chimamangidwa mozunguliranso (akuloza ziliza za mafumu ena pamandapo) osati chogona monga zina zimakhalira. Malo ano ndi a mafumu okhaokha komanso akazi awo. Mwana wa mfumu sagona pano pokhapokha ngati wavekedwa ufumu.

 

Kodi uku sikungovutika chabe?

Mwatero ndi inuyo koma ife sitiona kuvutika koma kukwaniritsa chikhalidwe chathu ndi ulemu kwa mafumu athu monga Angoni.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »