Chichewa

Mwangonde: Khansala wachinyamata

Listen to this article

 

Akamati achinyamata ndi atsogoleri a mawa, ambiri amaganiza kuti izi ndi nkhambakamwa chabe. Koma achinyamata ena, monga Lusubilo Mwangonde, akukwaniritsa akupherezetsa mawuwa osati pongolota kuti adzakhala, koma kutsogolera kumene chifukwa nthawi yawo yakwana. DAILES BANDA adacheza ndi Mwangonde, khansala wachinyama, yemwe akuimira Jumbo Ward mumzinda wa Mzuzu, motere:

Ali ndi masomphenya: Mwangonde
Ali ndi masomphenya: Mwangonde

Tikudziweni…                                                                                                   

Ndine Lusubilo Mwangonde, ndili ndi zaka 27 zakubadwa. Ndinabadwa m’banja la ana asanu ndipo ndine wachinayi kubadwa. Ndimachokera m’mudzi mwa Mwamalopa, kwa Paramount Chief Kyungu m’boma la Karonga. Sindili pabanja pakadalipano.

 

Mbiri ya maphunziro anu ndi yotani?

Maphunziro anga a pulaimale ndidachitira kusukula yapulaiveti ya Viphya mumzinda wa Mzuzu ndipo asekondale ndidachitira pa Phwezi Boys m’boma la Rumphi. Ndili ndi diploma ya Accounting ndipo pakadalipano ndikupanga digiri komanso Chartered Accounting kusukulu ya Malawi College of Accountancy (MCA).

 

Mudayamba bwanji zandale?

Kuyambira ndili wachichepere, zaka 12, ndakhala ndikukhala mumaudindo a utgogoleri. Ichi ndi china mwa zinthu zomwe zidandilimbikitsa kuti ndikhoza kudzapambana pazisankho. Koma chachikulu chomwe chidandichititsa kuti ndilowe ukhansala chidali chifukwa chakuti ndinkafuna kupereka mpata kwa anthu kuti azitha kuyankhula zakukhosi kwawo polimbikitsa demokalase ndi chitukuko.

Ntchito mukugwira ndi zomwe munkayembekezera?

Eya, ndiponso ndinkayembekezera zambiri.

 

Masomphenya anu ndi otani pandale?

Ine ndine munthu wokhulupirira Mulungu ndipo ndili ndi chikhulupiriro choti Iye ndi amene adzandionetsere zomwe ndikuyera kuchita ndi tsogolo langa.

 

Zinthu zina zomwe mumachita ndi chiyani pambali pa ukhansala?

Ndikakhala sindikugwira ntchito yaukhansala ndimakhala ndikuchita bizinesi, nthawi zina ndimakhala ndili kusukulu komwe ndikuchita maphuro anga a digiri. Kuonjezera pamenepo ndili ndi bungwe lomwe ndidayambitsa ndi anzanga ena la Centre for Participatory Democracy lomwe limalimbikitsa demokalase.

 

Zomwe mwakwanitsa ndi zotani?

Ndathandiza kuti ntchito yopala misewu ya kudera la Moyale itheke. Misewuyi yakhala nthawi yaitali osapalidwa. Ndidathandiziranso kuti ochita malonda ayambe kumanga mashopu anjerwa ndi kusiya kumangira matabwa kapena zigwagwa. Ndidakwanitsanso kukaimirira khonsolo ya Mzuzu ku Nyumba ya Malamulo. Ndaonanso kuti ntchitoyi yandithandiza kusintha momwe ndimaonera zinthu komanso ndimakumana ndi anthu osiyanasiyana omwe amandiphunzitsa zinthu zambiri.

Inu mukakhala mumakonda chiyani?

Ndimakonda kusewera mpira wa manja wa basketball.n

Related Articles

Back to top button
Translate »