Nkhani

Mwapasa achoke—HRDC

Listen to this article

Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party zati ziunika mwakuya ganizo la mgwirizano wa mabungwe omenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lomema aphungu kuti akakane Duncan Mwapasa kukhala mkulu wa apolisi.

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adasankha Mwapasa ngati ogwirizira mpandowo potsatira kupuma kwa yemwe adali paudindowo Rodney Jose yemwe wakwanitsa zaka zake zokapuma.

Ena akufuna kuti achoke: Mwapasa

Mwapasa akugwirizira mpandowo kudikira kuti aphungu a Nyumba ya Malamulo akaunike mbiri ndi luntha lake pankhani za chitetezo n’kuvomereza kapena kukana kuti mkuluyu akhale pampandowu.

Izi zili choncho potsatira zomwe ndime 154 (2) ya Malamulo a dziko lino imanena pakasankhidwe ka mkulu wa apolisi.

“Pulezidenti akuyenera kusankha mkulu wa apolisi pogwiritsa ntchito mphamvu zake koma Nyumba ya Malamulo ili ndi mphamvu zounika wosankhidwayo n’kumuvomereza kapena kukana. Akatero, komiti younika za kasankhidwe ka maudindo ya Public Appointments Committee (PAC) ikhoza kuunika kagwiridwe ntchito ka mkulu wa apolisiyo nthawi iliyonse,” akutero malamulo.

Koma wachiwiri kwa wapampando wa HRDC Gift Trapence adati akuona ngati Mwapasa sangatsogolere bwino apolisi chifukwa amaoneka kuti amagwirizana ndi chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) kotero sangatsogolere apolisiwo.

Iye adati pachifukwachi, bungwelo lakonza zomema aphungu a Nyumba ya Malamulo kuti asakamuvomere Mwapasa akamakumana podzakambirana za ndondomeko ya zachuma ya 2019/2020 mwezi wa mawa.

“Mwapasa ndi wa DPP kutanthauza kuti chilichonse amapanga nchokomera chipani cha DPP. Kukhala mkulu wa apolisi, ndiye kuti polisi isanduka chida cha DPP mmalo mokhala chida cha Amalawi,” watero Trapence.

Mwapasa adakana kulankhulapo pa nkhaniyi pocheza ndi nyuzipepala ya The Nation Lolemba HRDC itangolengeza ganizo lake pa msonkhano wa atolankhani.

Mneneri wa MCP Maurice Munthali wati chipanicho chili n’chikhulupiliro mwa aphungu ake kuti akaona zochita nthawiyo ikadzafika pomwe mneneri wa UTM Party Joseph Chidanti Malunga adati chipani chiona zochita HRDC ikachipeza.

“Poti iyi ndi nkhani ya ku Nyumba ya Malamulo, tiyisiya mmanja mwa aphungu athu omwe tili nawo chikhulupiliro chonse kuti akaunike Mwapasa mopanda mantha kapena kunyengereredwa. Nthawi yopatsirana maudindo patebulo idatha,” adatero Munthali.

Ndipo Malunga adati: “Padakalipano sitinena zambiri koma a HRDC akatipeza nayo nkhaniyi tidzayilandira n’kupanga chiganizo mozama kuti Amalawi asataye chikhulupiliro mwa ife.”

Katswiri pa ndale George Phiri wati ndondomeko yosankhira mkulu wapolisi ndi yomveka bwino ndiye ngati HRDC yaonapo vuto ndi Mwapasa, zili ndi iwo kutengera nkhawa zawo kwa aphungu.

“Pulezidenti wasankha, koma zonse zikutsalira aphungu ku Nyumba ya Malamulo. HRDC ikawapatse nkhawa zake ndipo aphunguwo akaona kuti akatani pa nkhawazo. Koma khulupilirani kuti ngati Mwapasa wasankhidwira ndale kapena mtundu, akavutika kudutsa,” watero Phiri.

Nyumba ya Malamuloyi ikakakana Mwapasa ndiye kuti akhala munthu wachiwiri kukanidwa ndi nyumbayo kukhala mkulu wa apolisi kutsatira kukanidwa kwa Mary Nangwale mu 2006 yemwe adasankhidwa ndi mtsogoleri wakale Bingu Wa Mutharika.

Aphungu ataunika maiyo adaona kuti samakwanira kutsogolera nthambi ya apolisi ndipo adamukana n’kuunikira kuti Mutharika asankhe munthu wina woti atsogolere nthambi ya apolisi.

Mwapasa wakhalanso mdindo wachiwiri yemwe bungwe la HRDC silikufuna akhale pampando kutsatira wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah yemwe pakali pano HRDC ikutsogolera zionetsero zoti atule pansi udindo wake.

Related Articles

Back to top button
Translate »