Nkhani

Mzomera wadzipereka m’manja mwa apolisi

Gavanala wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) m’chigawo chakumpoto Christopher Mzomera Ngwira wadzipereka m’manja mwa apolisi Lachinayi.

Mzomera, yemwe watuluka pa belo tsiku lomwelo, akumuganizira kuti akukhudzidwa ndi zaupandu zomwe achinyamata a DPP adachitira atsogoleri otsutsa boma pa bwalo la Chibavi ku Mzuzu pa March 20 2016.

Wadzipereka: Mzomera Ngwira

Mtsogoleri wa Malawi Congress Party (MCP) Lazarus Chakwera adachititsa msonkhanowo mogwirizana ndi atsogoleri a zipani za Alliance for Democracy (Aford) Enock Chihana ndi wachiwiri kwa mkulu wa chipani cha People’s Party (PP) Kamlepo Kalua.

Anyamata a DPP adasokoneza msonkhanowo, kukhapa anthu atatu ndi phwitika, komanso kuononga katunda wambiri.

Apolisi akhala akufunafuna mkuluyu kuyambira sabata yatha, koma samapezeka.

Mneneri wa polisi m’chigawocho, Peter Kalaya, adatsimikiza kuti Ngwira wadzipereka m’manja mwawo.

Pokadzipereka, Ngwira adali ndi womuyimira pa milandu Christon Ghambi yemwe masiku apitawo adatsutsa malipoti woti mkuluyu akuthawa.

“N’zoona kuti lero [Mzomera Ngwira] anabwera ndi womuyimira pa milandu ndipo tamumanga poyembekezera kupita naye ku khoti,” adatero Kalaya.

Naye Ghambi adatsimikiza kuti Ngwira wadzipereka ndipo wamangidwa.

“Sindilankhula zambiri kaamba koti ndikufuna kukamupemphera belo ndipo ndikudikira kumva zomwe khoti linene,” adatero Ghambi.

Otsatira DPP adapita ku khoti komwe amayimba nyimbo zoti Mzomera Ngwira amutulutse.

Ena mwa akuluakulu a chipanichi omwe adapita ku khotiko ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa DPP m’chigawo cha kumpoto Goodall Gondwe ndi msungichuma wa chipanichi, Jappie Mhango.

Gondwe adati wafika ku khotiko kukamulimbitsa mtima Ngwira, koma adakana kuthirirapo ndemanga pa mlandu wake.

Ena mwa achinyamata a DPP omwe amangidwa mokhudzidwa ndi mlanduwu ndi Big Joe, George Mwamtobe, Lumbani Munthali ndi Thembisile Nkosi.

Anthuwa akuimbidwa mlandu woyambitsa chiwawa, kuvulaza anthu ndi kuononga katundu.

Related Articles

Back to top button