Nkhani

Namrukhunua: Nyumba ya chilhomwe

Listen to this article

Kalelo makolo adali ndi njira zawo zochitira zinthu kuti azisangalala ndi kukhala wotetezedwa. Alhomwe nawo ali ndi zimene makolo awo adayambitsa

ndipo zina zimapitirirabe mpaka pano. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wotsata chikhalidwe cha Alhomwe mumzinda wa Lilongwe, Fustafu Mbewe. Adacheza motere:Namrukhunua

Pa mtundu wa Alhomwe pali mawu akuti ‘Namurukhunua’, kodi tanthauzo lake nchiyani?

Imeneyi ndi nyumba yozungulira yomwe makolo pa mtundu wa Chilhomwe adayambirira kumanga kalelo nkumakhalamo. Kanyumba kameneka kamakhala kakang’ono ndipo kamakhala kopanda chipinda.

 

Pomanga amagwiritsa ntchito zipangizo zanji?

Timagwiritsa ntchito mitengo, tsekera, khonje, zilambe, matope ndi namgoneka (zokhala ngati zilambe ndipo ena amalukira mipando). Masiku ano enanso amagwiritsa ntchito misomali. Chitseko chimakhala cha kaphe, kabala wake mtengo omwe umapingasa pachitseko.

 

Ndiye mwati imakhala nyumba yaing’ono, mumakhala anthu angati mmenemo?

Namrukhunua mumakhala anthu awiri (banja) ndipo ngati pali wachitatu ndiye kuti ndi mwana wa m’nyumbamo. Ngati pali anthu ambiri, amamanganso tinyumba tambiri pamodzimodzi ngati banja limodzi koma katundu yense wakukhitchini, ziwiya za madzi ndi madengu a ufa amakhala m’nyumba momwemo.

 

Pomanga zimakhala bwanji?

Pamalo akasosapo bwinobwino amatenga chingwe ndi mitengo nkuyamba kuyeza muja amachitira akafuna kumanga nkhokwe. Akakwanitsa kupimako, amazika mitengo mmphepetemo ndikuyamba kuphoma ndi matope ndipo akamaliza amafolera ndi tsekera nkukonza chitseko.

 

Pachibale pawo akalakwirana nkhani zake zimayenda bwanji?

Monga ndanena kale, pachibale amamanga nyumba zawo pamodzimodzi kupatula makolo, omwe amamanga patali pang’ono koma poonekera ndiposavuta kufikapo. Pakachitika mapokoso, amakauza makolo olo ngati zili za m’banja, amauza ankhoswe ndikukamba koma zikalephera ndiye zimakafika kwa amfumu kuti athandizepo.

 

Nanga amuna a Chilhomwe zida zawo ndi chiyani?

Alhomwe zida zawo ndi chikwanje (koma chimakhala ndi ngowe), nsompho (nkhwangwa) ndi mpeni omwe amautchinjiriza ndi kachikwama kopangidwa ndi chikopa cha nyama. Mpeni wa Mlhomwe suonekera chisawawa amaubisa ndipo umatuluka pokhapokha ngati ukufunika kuti ugwire ntchito.

 

Alhomwe ntchito yawo yaikulu ndi chiyani?

Alhomwe amakonda kulima. Mbewu zomwe amakonda kulima kwambiri ndi kalongonda, chinangwa, nandolo, mbatata, nzimbe, chimanga, mapira ndi tchana. Chakudya chawo chodalilika ndi nsima ndi zipatso; amakondanso nandolo osakaniza ndi makaka.

 

Nanga mavalidwe awo?

Amayi a Chilhomwe amakonda kuvala nsalu, andiloko (iyi ndi siketi yaitali yomwe ena amati makisi), bulauzi ndi mpango ndipo amakonda kusokera nsalu ya biliwita (yakuda). Abambo amakonda kabudula ndi malaya osokedwa ndi nsalu ya khaki.

 

Tangomalizani ndi ena mwa magule otchuka pa chilhomwe.

Pali magule monga tchopa, sekhere ndi jiri. Povina Tchopa amavala zikopa za nyama komanso amaberekera tinthu tokhala ngati nyama kumsanaku m’miyendo muli mawerewesa oti azipanga kaphokoso povina. Povina sekere amavala mikanda paliponse ndi m’khosi momwe komanso amadzikongoletsa nkhope yonseyi. Jiri ndi gule yemwe amavinidwa usiku kuli mwezi ndipo amavina ndi amuna ndi akazi. Mwachidule magule ndiye alipo ambiri osangalatsa pa mtundu wa Alhomwe.

Related Articles

One Comment

  1. Nyumba izi za “namurukunuwa” sizioneka kwambiri kuno ku Malawi, masiku ano. Koma ku Mozambique ndiyetu eee zambiri. Nthawi yotentha ngati ino, namurukunuwa samatentha ngati nyumba za makona (rectangular houses).Ndipo zimapasuka pa mphepo ya mphamvu kwambiri yokhaokha baasi. Osati pa mphepo ya masewela.
    Mitundi ina ya anthu, pa ziko lapansi pano, monga ma esikimo ndi “amwenye” (native indians) a ku Canada, amamanganso nyumba ngati zimenezi.
    Pa za ulimi: tinene kuti aLhomwe zonsezi anaphunzira ku malo oyambira kumene anakhala poyamba kuchokela ku Congo kuja, pa mtundo wawo wa aMakuwa. Cha m’ma 500AD. Ku Namulhi – kuphiri kuja kudela la Zambezia, ku Mozambique – kunthaka yamphanvu ngakhale ulibe feteleza.
    Apa tinenenso kuti lhomwe kutanthauza kwace ndi nthaka (“lhomwe” means “soil”). Ndipo ndichifukwa alomwe ambiri amaziona ngati ndi ma dolo a zolima.

Back to top button