Nkhani

Nanawa: Mlowam’malo wa kupitakufa

Listen to this article

 

Matenda a HIV/Edzi asokoneza miyambo ina monga mwambo wa kupitakufa, womwe umapereka mphamvu kwa ‘fisi’ kuti akakonze maliro pocheza ndi namfedwa kwa sabata ziwiri ndipo machezawo amachitika katatu patsiku. Chifukwa cha matendawa, kwabwera njira ya nanawa yomwe yazilalitsa mwambo wa kupitakufawu. BOBBY KABANGO adali m’boma la Nsanje komwe adacheza ndi mlembi wa nyakwawa Masanzo kwa T/A Mlolo.

Kodi amfumu tawapeza?

Ayi, iwowa adzukirira kudimba. Akuyembekezereka kubwerako madzulo chifukwa ntchito yakula kumeneko.

 

Tidalire kuti inu mutithandiza pa vuto lathu?

Musakaikenso, ndine mlembi wa amfumuwo ndiye palibe chomwe sindikuchidziwa chokhudza mudzi uno ndi miyambo yomwe timatsata.

Mkaka: Mwambo wa nanawa timangomwa  mankhwala othamangitsa imfa
Mkaka: Mwambo wa nanawa timangomwa
mankhwala othamangitsa imfa

Kodi mwambo wa kupitakufa ukuchitikabe kuno?

Zikuchitika koma mobisa chifukwa momwe matenda a Edzi aopseramu sungayerekeze kumachitabe mwambowu. Amabungwe akhala akufika kumemeza anthu kuti miyambo yoipa, monga umenewu, itheretu ndipo zipatso zake zikuonekadi pano.

 

Ndiye mukutani kuti imfa ithawe pakhomo?

Timagwiritsa mankhwala a ‘nanawa’ amene amathamangitsa imfa pakhomo. Kuno anthu ambiri tikutsata zimenezi.

 

Nanawa n’chiyani?

Ndi mankhwala amene sing’anga amachita pakhomo pamene pagwa maliro. Anthu, maka achibale, amamwa mankhwalawo molandirana ndipo pakhomopo pamakhala bwino.

 

Zimachitika nthawi yanji?

Maliro akachitika monga lero, mawa timakaika ndiye timasweretsa tsiku limodzi pamene timasonkhana kudzasesa. Nthawi yosesa mpamene mwambo wa nanawa umachitika. Mungathe kuchita mwambowu nthawi iliyonse kaya ndi masana kapena madzulo.

 

Kodi mankhwalawa mumatemera kapena mumadya?

Mankhwalawa ali pawiri. Ena amakhala a madzi. Amawaika m’kapu ndiye aliyense wachibale amalandirana mankhwalawo kumamwa pang’ono mpaka nonse achibale akukwaneni. Pamene mankhwala ena amawaika kudenga kwa nyumba yomwe mumagona malemuwo. Mumawasomeka kudenga mbali yomwe kuli khomo kuti anthu akamalowa m’nyumbamo azigwira mankhwalawo.

 

Mukutanthauza wachibale aliyense amayenera amwe mankhwalawo?

Zimatero kumene. Nonse mumalandirana, kumwa pang’ono basi, aliyense kamodzi komanso momapatsirana.

Nanga achibale amene sadafike pamwambowo mumawatani?

Achibale amene nthawi ya malirowo kapena tsiku la kusesalo palibepo, timawasungira mankhwalawo. Mankhwala ake ndi amene tawasomeka kudenga aja. Tsiku lomwe akonza zodzafika pakhomopo, timawalandira ndi kuwatengera kunyumba yomwe kudachitika malirowo. Ndiye pamene tikulowa m’nyumbayo, timawapatsa mankhwala aja kuti agwire. Akangotero basi amabwezeretsa mankhwalawo kudengako.

 

Amachitanso china chiti?

Palibe, ngati agwira mankhwalawo ndiye kuti nawonso akonzedwa ku imfa yomwe idakangogwa pakhomopo.

 

Nthawi yomwe munkatsata mwambo wa kupitakufa zinkakhala bwanji?

Maliro akachitika chonchi, timapeza fisi kuti apite kunyumba yomwe kwachitika malirowo akacheze ndi namfedwayo. Katatu patsiku kapena zikavuta atha kumacheza nawo kawiri patsiku kwa sabata ziwiri. Fisiyu ntchito yake idali yoti achotse mzimu wa imfa womwe wakuta pakhomopo.

 

Mpaka katatu? Ndiye zidalikolikotu…

Hahaha! Eeh, amasangalala kwambiri koma pano zimenezi zidatha.

 

Nanga akamwalira wamkazi, afisi aakazinso amapezeka?

Ayi, zikatere ndiye tinkapanga mankhwalawa kapena apo ayi mupemphe banja lina kuti likupitireni kufako.

Related Articles

Back to top button