Chichewa

Ndaziona: Aona kuwala ku Mozambiki

Listen to this article

Mwezi wathawu osewera awiri, Ndaziona Chatsalira ndi Green Harawa adachoka ku Silver Strikers ulendo ku Mozambique kukasaka moyo wina. Chatsalira wauza BOBBY KABANGO kuti ku Mozambique kuli mkaka ndi uchi ndipo wayamba kumva kukoma. Zakoma bwanji kodi? Kucheza kwawo kuli motere.

Ali ku Mozambique: Chatsalira
Ali ku Mozambique: Chatsalira

Wawa mbale wanga, zikuyenda kumeneko?

Inde achimwene. Ku Malawi kuli bwanji?

Pang’ono, chimanga chikusowa, kaya kumeneko?

Kuno tonse tilipo, ine ndi mnzanga Green Harawa zonse zikuyenda ndipo pagalaundi zonse zili bwino.

Chili bwino nchiyani?

Mukudziwanso kuti timu ya Ferroviarrio de Nampula si timu yaing’ono, ndiye ukamapatsidwa mpata kuti uonetse luso lako anthu ndi kumayamikira zimatanthauza zambiri.

Kodi ligi yanu iyamba liti?

Iyamba mu March moti zokonzekera zili mkati. Panopa tili m’njira ulendo ku South Africa kukachita zokonzekera koma matimu amene tikukasewera nawo sadatiuze.

Zokonzekera zikuyenda bwanji?

Zonse zili bwino, tachita nawo zokonzekera kwa sabata ziwiri, anthu akuyamika.

Wachita chiyani kuti ayamikire?

Zigoli, ndakoleka kale zigoli 10. Nayenso Harawa wachinya 15 ngati sindikulakwa.

Ukusewera malo ati kuti mpaka uchinye zigoli 10?

Pakati cha kumanzere pena kumanja koma mokagundagunda pagolo.

Kumeneko ndiye ukutchedwa ndi dzina liti?

Da Silva Chatsalira chifukwa ndikuvala jersey nambala 21. Mukudziwanso kuti ndimakonda da Silva wa Manchester City.

Ndalama mukulandira motani?

Malipiro ali bwino kwambiri koma sindinganene momwe tikulandirira. Chilichonse chokhudza mpira kuno chili bwino kusiyana ndi kwathuko. Mbali zonse tingonena choncho kuti zili bwino kuyerekeza ndi kumudziko.

Tsogolo ukuliona bwanji?

Lowala, amwene, ndipo tigwira ntchito modzipereka kuti anthu adziwenso kuti kuli Chatsalira ndipo matimu ena ationa ntchito yomwe tigwire. n

Related Articles

Back to top button
Translate »