Chichewa

Ndege ya ufiti’ ikodwa ku Kasungu

Listen to this article

Ngakhale malamulo a dziko lino amakana kumutchula munthu kuti ndi mfiti, Amalawi ambiri amakhulupirira kuti ufitu uliko.

Anthu a m’mudzi mwa Gundani m’boma la Kasungu adodoma ataona chinthu chooneka ngati ndege chomwe akuchiganizira kuti ndi ndege ya afiti chitagwa m’mudzimo.

The alleged witch craft plane that crashed

 

Msangulutso utafufuza chomwe chidachitikita, udapeza kuti ‘ndegeyo’ idagawa pakhomo pa Yusufu Abubaka Ali yemwe akukhulupilira kuti akola mfiti zomwe zakhala zikusautsa banja lawo.

“Anthu amenewa adalodza akazi anga koma ndi mmene agwidwiramu akazi anga akhala bwino,” adatero Ali.

Mkazi wa bamboyo Liness Kaulongo wakhala akudwala kwa nthawi yaitali ndipo kuchipatala cha boma ku Kasunguko adawauza akayesere zachikuda.

“Tidapita kwa asing’anga komwe adationetsa anthu anayi kuti ndi omwe akusautsa banja lathu. Sing’angayo adatipatsa mankhwala omwe adati tikaike panyumba yathu kuti ndidzakole mfiti zomwe zimanditambilazo,” adatero Ali.

Iye adati sanadabwe kwambiri mkazi wake akuuza kuti kunja kwa nyumba yawo kwagwa chinthu chooneka ngati ndege.

Kaulongo, adati adadabwa kuona chinthu chamaonekadwe ngati ndege chili panja panyumba yayo pomwe adatuluka usiku kukataya madzi.

Mneneri wapolisi m’boma la Kasungu Edwin Kaunda adatsimikiza kuti iwo akusungadi chinthu chomwe chikuganiziridwa kuti ndi ndege yaufiti.

Iye adati adapita pamalopo kukakhazikitsa bata chifukwa chinthucho chinkabweretsa mpungwepungwe pa malopo.

“Ife tidapita kukatenga chinthucho ndipo tili nacho kuno kupolisi,” adatero Kaunda.

Related Articles

Back to top button