Chichewa

Ndi ana omwe akudzipha

Bambo wina adadzipha m’boma la Chiradzulu atazindikira kuti mkazi wake amachita ubwenzi wa mseri ndi mchimwene wake.

Izitu zidaululika pomwe awiriwo adapita kuphiri kukapemphera ndi mbusa wina ndipo kumeneko adayamba kuulula machimo awo.

Malinga ndi omwe adatitsina khutu pa nkhaniyi, Tendai Black adali pabanja ndi mphunzitsiyo Malango Patani ndipo adapita kuphiri la Chiradzulu kukapemphera, kwinaku akusala kudya ndi mbusayo.

Nkhani zodzipha zili paliponse m’dziko muno.

Kuonekera m’bwalo lamilandu chifukwa chofuna kudzipha

Sabata yatha yomweyo, Mfumu Pasani ya kwa Mfumu Yaikulu Kapeni m’boma la Blantyre nayo idadzipha.

Komatu chodabwitsa n’choti ngakhale nawo ana akudzipha.

Mwachitsanzo, mwana wina wa zaka 12 adadzipha ku Mponela, m’boma la Dowa atadzudzulidwa ndi mayi ake.

Malinga ndi mneneri wa polisi ku Mponela, Kaitano Lubrino, mwanayu adapezeka atadzimangilira m’munda wa soya.

“Mayi amwanayu adakagula tiyi ndi kumumana mwanayu ngati chilango chifukwa chosadyetsa phala mphwake pomwe mayiwo adachoka,” adalongosola Lubrino.

Mwanayo amachokera m’mudzi mwa Katuta, T/A Kayembe. m’boma la Dowa.

Polankhulapo, wachiwiri kwa mneneri wa polisi m‘dziko muno Peter Kalaya adati mchitidwe wodzipha wakhala ukukula kuchokera chaka chatha.

Kalaya adati pomwe m’chaka cha 2019, anthu 178 adadzipha, chaka cha 2020 anthu omwe adadzipha adalipo 270. Izi zikutanthauza kuti chiwerengerochi chidakula ndi anthu 52 mwa 100 alionse.

“Tsiku lililonse timalandira lipoti loti munthu kapena anthu adzipha,” adatero Kalaya.

Iye adati anthu 90 mwa 100 odzipha ndi abambo, pomwe amayi odzipha ndi ochepa ndipo ndi 10 otsalirawo.

Kalaya adatinso kafukufuku wa apolisiwa wakhala akuonetsa kuti ambiri amadzipha chifukwa cha mavuto a m’banja ndi zachuma mwa zifukwa zina.

Malinga ndi kafukufuku yemwe adapanga Gift Banda komanso Natasha Banda ndi anzawo ena awiri ndipo adasindikizidwa pa January 21 mu Panafrican Med Journal, kudzipha kwafika poipa m’dziko muno ndipo sikudasiye mbali.

Kafukufukuyu adapeza kuti anthu ambiri, maka abambo, akudzipha chifukwa cha nkhawa zosiyanasiyana, kuphatikizapo umphawi.

Kafukufukuyo adapemphanso atolankhani kuti akamalemba nkhani zokhudza kudzikhweza asamalongosole mwachindunji momwe zidakhalira.

Pamapeto pa zonse kafukufukuyo adati dziko lino liyambe kuika patsogolo matenda a kaganizidwe chifukwa mmene zilili panopa, zaumoyo za dziko lino sizingakwanitse kuthana ndi mliliwu.

Pomwe katswiri pankhani zounika za kaganizidwe (clinical psychologist) kuchokera ku Saint John of God Ndumanene Silungwe adati chiwerengero cha anthu omwe akudzipha chitha kukhala kuti chikukwera chifukwa cha nyengo ya Covid-17 yomwe dziko likudutsamo.

“Nyengo ya mliri yabweretsa nkhawa, imfa, kuvuta kwa chuma ndi zina zomwe zikuchititsa kuti anthu adziphe chifukwa cha kusintha kwa moyo,” adalongosola Silungwe.

Pa ana omwe akudzipha,Silungwe adati sizimachitikachitika ana kudzipha koma zikatero zimakhala kuti anawo sakumvetsa kwenikweni zomwe akuchita kapena kuti adaonera pa kanema kapena kuwerenga mmene anthu amadziphera ndipo nawo adangotengera zomwezo.

“Akakhala ana okhwimirako ambiri amadzipha chifukwa choti maubwenzi awo atha kapena akhumudwitsidwa ndi okondedwa awo,” adalongosola Silungwe.

Iye adatinso pothana ndi vutoli n’kofunika kumagawana nkhawa ndi anthu omwe angawamasukire komanso kupita kuchipatala ngati munthu akuona kuti sizikuyenda bwino pakaganizidwe.

“Munthu akamanenanso kuti adzipha, tisamanyozere uthengawo,” adalongosola Silungwe.

Related Articles

Back to top button