Chichewa

Ndi Walter, Mijiga Kapena Yabwanya?

Listen to this article

 

Atatsatsa mfundo zawo masiku apitawa, omwe akulimbirana maudindo kubungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo la Football Association of Malawi (FAM) akhala akukumana maso ndi maso pazisankho zomwe zikuchitika lero.

Nthumwi zokwana 36 zochokera kunthambi za FAM ndi zomwe zitaponye voti pamsonkhano waukulu womwe ukuchitikira m’boma la Mangochi.

Akuimanso: Nyamilandu
Akuimanso: Nyamilandu

Omwe akupikisana paudindo wa pulezidenti ndi yemwe pakalipano ali pampandowu, Walter Nyamilandu, Wilkins Mijiga komanso a Willy Yabwanya Phiri.

Akuluakuluwa sabata yathayi adali kalikiriki kupereka mfundo zawo pazomwe akufuna adzachite akasankhidwa paudindowu.

Polankhula mumzinda wa Lilongwe, Nyamilandu adalonjeza kuti akapambananso adzakhazikitsa ndondomeko zoonesetsa kuti mpira wa m’makwalala ukupita patsogolo komanso kuti mpira ukubweretsa ndalama zochuluka maka m’makalabu osiyanasiyana.

Wakonzeka: Mijiga
Wakonzeka: Mijiga

Kumbali yake Yabwanya adalonjeza kuti adzasula aphunzitsi a mpira ambiri omwe azitha kuphunzitsa anyamata achisodzera ndi cholinga choti luso lawo lipite patsogolo.

Naye Mijiga pomema anthu kuti amusankhe, adati adzakhazikitsa njira zopezera ndalama ndi cholinga choti osewera, oyimbira komanso oyendetsa mpira azilandira ndalama zambiri.

Pakalipano zikuonetsa kuti Nyamilandu atha kutenganso mpandowu kaamba koti mwa nthambi zisanu ndi zinayi za bungwe la FAM, zisanu ndi ziwiri zidalengezetsa kuti zili pambuyo pake.

Ali momo: Yabwanya Phiri:
Ali momo: Yabwanya Phiri:

Nthambi imodzi yokha ya Super League of Malawi ndi yomwe ikuti ili pambuyo pa Mijiga pomwe ya National Referees Committee ndi yomwe ikuti ili pambuyo pa Yabwanya. Koma zioneka komweko chifukwa voti ikhala yachinsinsi.

Omwe akupikisana pampando wa wachiwiri kwa pulezidenti ndi Tiya Somba-Banda ndi James Mwenda. Mpikisano pampando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa pulezidenti uli pakati pa Pikao Ngalamila ndi Othaniel Hara.

Ndipo omwe akulimbirana kuti akhale mamembala a komiti yaikulu ya FAM ndi Jabbar Alide, Alfred Gunda, Masauko Medi, Hubert Mfune, Daud Mtanthiko, Flora Mwandira ndi Rashid Ntelera. n

Related Articles

Back to top button