Chichewa

‘Ndidadabwa ndi dzina lake’

Dzina loti Mpunga lidadabwitsa njoleyo. Poti akatsimikize ngatidi dzinalo lidali la munthu, adakakumana ndi mbalume za bamboyo ndipo tikunenamu apangitsa chinkhoswe ukwati ulipo August akudzayu.

Awa ndiye makumanidwe a Victor Mpunga wa kwa Chikowi m’boma la Zomba ndi Shilla Gobede wa m’mudzi mwa Nsiyaludzu kwa Makwangwala ku Ntcheu.

Victor ndi bwenzi lake Shilla

Victor adati njira yokamupezera Shilla idali mwa mchemwali wake amene amagwira naye ntchito ku m’boma la Nkhotakota.

“Apa sindimadziwa kuti Shilla ali ndi mbale wake amene mawa angadzakhale mkazi wanga.”

Tsiku lina Victor akuti adayendera munda wake ku Lilongwe. Chipemba cha madzi chidamugwira ndipo adazindikira kuti pafupi ndi munda wake kumakhala mchemwali wa Shilla.

Adapita kuti akamwe madzi. Madzi adamwa, ludzu la madzi lidatha, koma ataona Shilla, ludzu lofuna kudzatenga namwaliyo ngati mkazi wake lidamugwira.

“Mchemwali wanga adandiuza kuti kwabwera Mpunga, dzinalo lidangondisangalatsa ndipo ndidapita kuti ndikamuone munthu wotchedwa Mpungayo,” adatero Shilla.

Kuyambira pomwepo akuti awiriwo adasinthana manambala ndipo adayamba kuchezerana. Mosakhalitsa mawu adatsokoloka ndipo mu February 2018 Shilla adalola.

Awiriwo akukhala ku Lilongwe komwe Shilla akuphunzitsa ku sukulu, komanso kuchita sukulu yake ya utolankhani ku Malawi Institute of Journalism (MIJ).

“Chidandikopa ndi ulemu komanso kulankhula modekha kwa Shilla,” adatero Victor. “Komanso amapezeka malo osakayikitsa nthawi zonse.”

Ukwati wa awiriwo ulipo pa 18 August chaka chino ku Lilongwe. n

Related Articles

Back to top button