Nkhani

Ndikakunyenyani kukovenshoni—APM

Listen to this article

Pamene chipani cha DPP chalengeza kuti msonkhano waukulu ulipo mwezi wa mawa, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika Lachinayi adati anthu amene akufuna kukapikisana naye kukovenshoni yachipanicho akawakhambitsa ndi kuwagonjetsa.

Polankhula pomwe amakhazikitsa mwala wa maziko pamsewu wa Lirangwe-Chingale-Machinga pasukulu ya Lifidzi m’boma la Blantyre, Mutharika amene akufuna kukapikisana naye pampando wa oimira chipanicho ndi opusa.

Zonse zikuyenda: Chilima ndi Mutharika pa kampeni ya 2014

“Mumafuna kuvenshoni lero talengeza ilipo, inu mukuti mukatenga chiletso kukhoti. Ndinu opusa kwambiri, mukuopa chiyani? Kukovenshoni ndikakufinyani, ndikakupondapondani ndipo ndikakunyenyanyenyani,” adatero Mutharika.

Nthawi yomwe Mutharika amalankhula izi n’kuti gulu limene lakhala likumema Chilima kuti adzapikisane ndi Mutharika likuchititsa msonkhano wa atolankhani komwe adapempha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyo adzapikisane ndi Mutharika.

Pamsonkhanowo padafikanso mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Callista Mutharika yemwe kumayambiriro kwa mwezi wa April ndiye adavumbulutsa nkhani yoti Peter asadzaimire DPP, mtsogoleri wa amayi mu DPP Patricia Kaliati, phungu wa kumwera m’boma la Mulanje Bon Kalindo, mwa atsogoleri ena.

Powerenga chikalata cha gululo, Kaliati adati akupempha Chilima kuti adzapikisane ndi Mutharika chifukwa waphwanya chipangano.

“Chisanachitike chisankho cha 2014, Mutharika adaneneratu kuti adzangolamulira zaka 5 ndiye lero bwanji akukakamira kuti adzaimirenso? Tikuona kuti Mutharika akumvera kwambiri anthu ena amene akumupusitsa, anthu amene nthawi yomwe tinkazunzika adathawa ndipo amafalitsa mabodza kuti Mutharika asaime,” adatero Kaliati.

Iye adati iwo akungotsatira ndime yachiwiri ya gawo 10 ya malamulo oyendetsera DPP imene imati akuluakulu a chipanicho ayenera kusankhidwa pakatha zaka 5.

“Tikudabwanso kuti Mutharika sanaitanitsepo msonkhano wa akuluakulu a chipanicho monga chipani chimayendera. Mkhumano wotere umayenera kuunikira ngati chipani chikutumikira bwino Amalawi,” adatero Kaliati.

Kuchokera pomwe Callista adanena kuti Mutharika asadzaimire DPP, mkokemkoke wayala nthenje mu DPP pomwe gulu lina likufuna Chilima pomwe ena akuti koma Mutharika.

M’sabatayi Mutharika adakumana ndi Chilima koma zomwe adakambirana sizikudziwika. Kukumanako kudachitika pasanathe sabata kuchokera pamene nduna zitatu—Goodall Gondwe, Samuel Tembenu komanso Bright Msaka—zidakumananso ndi Chilima.

Malinga ndi akadaulo ena a ndale, kuchedwa kochititsa msonkhano waukulu wa chipanicho kumadzetsa mavuto ndipo kumasokoneza ovota.

Katswiri wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Livingstonia University George Phiri adati kuchedwa kwa DPP kuchititsa msonkhano waukulu kuti uthane ndi mkangano wa Mutharika ndi Chilima kudali ngati kudzimenya.

“Pandewu munthu sangapambane ngati akudzimenya yekha chifukwa mdani wako amapezerapo danga. Chodabwitsa n’choti zipani sizikulingalira za nkhaniyi koma nthawi ikupita,” watero katswiriyu.

Koma mlembi wamkulu wa DPP Grezeldar Geoffrey Lachitatu adalengeza kuti msonkhano waukulu wa chipanicho ulipo mwezi wa mawa.

“Aliyense amene akufuna kukapikisana nawo pamipando yonse yaikulu ya chipanichi. Msonkhanowo udzachitika ku Blantyre koma malo ndi tsiku lenileni adzalengeza ndi wapampando wa msonkhanowo,” adatero Jeffrey.

Padakalipano, zipani za MCP ndi Aford zidachititsa kale misonkhano yake yaikulu pomwe UDF ikuti idzachititsa msonkhano wake pa 1 August. Chipani cha PP sichinanene tsiku limene chidzachititse msonkhano wake.

Related Articles

Back to top button
Translate »