Chichewa

‘Ndimafuna mwamuna wadzitho’

Listen to this article

 

Felix Mwamaso ndi mmodzi mwa akatswiri osewera nkhonya mdziko muno. Koma kuti zonse zizimuyendera tayale choncho pali nthiti yake, Queen, yemwe amamuchengeta. Koma nanga awiriwa adakumana bwanji?

“Ndinkafuna mwamuna wadzitho, nthawi zonse ndinali kudikirira kuti ndidzapeze wamaonekendwewa. Nditamuona Felix akuponya maso pa ine panthawi ya nkhonya yake ku Obrigado Leasure Park mumzinda wa Mzuzu, ndinati mwayi suposa apa,” adatero Queen polongosola mmene adakumanirana koyamba ndi mwamuna wake.

Adayanjana magazi: Queen ndi Felix Mwamaso
Adayanjana magazi: Queen ndi Felix Mwamaso

Kuchokera panthawi imene adaonana pamalo ankhonyawa mu August chaka cha 2013, awiriwa adagwa m’chikondi chozama ndipo kenako adamanga banja chaka chomwecho mwezi wa November.

“Malinga ndi maongokedwe ake, Queen adandipatsa chikoka choti ndimutengere panyumba. Mwamwayi nditaponya mawu oti ndamukonda sadavute, ndipo ndidazitenga kuti ndi zomwe amayembekezera,” adatero Felix.

Awiriwa akukhalira limodzi ku tauni ya Chibavi ku Mzuzu.

Lachitatu sabata yatha, chisangalalo chokumbukira kuti akwanitsa zaka zitatu ali limodzi ngati banja chidali cha mtima bii ndipo chidachitikira pamalo ena achisangalalo ku Mzuzu otchedwa Sports Cafe.

Queen amachokera m’mudzi mwa Kayeleka, kwa Inkosi ya Makhosi (Paramount Chief) M’mbelwa m’boma la Mzimba pamene Felix ndi wa m’mudzi mwa Mwanjawale, Mtemi wa Matemi (Paramount Chief) Kyungu m’boma la Karonga. n

Related Articles

Back to top button
Translate »