Chichewa

‘Ndinkafuna mkazi wamakhalidwe’

 

Ronald Mwandama amene amakhala m’dera la Bangwe ku Blantyre adakhala zaka ziwiri wopanda wapambali atamwalira mkazi wake. Mu 2014 adapalana ubwenzi ndi Annie Kalambo yemwe amachokera m’mudzi mwa Sayiko, T/A Santhe m’boma la Kasungu, yemwe nayenso bambo wakunyumba adatsikira kuli chete.

Ronald akuti adali akuwunguza mkazi woti amange naye banja kutsatira imfa ya mkazi wake ndipo samangofuna munthu wamba koma mkazi wamakhalidwe abwino.

Ronald ndi Annie pano ndi thupi limodzi
Ronald ndi Annie pano ndi thupi limodzi

“Pafupi ndipo uli. ndinasaka mu Bangwe momwemuno mkazi wamakhalidwe omwe ine ndimafuna. Pomuona Annie, mtima unakhutira ndipo ndinayamba kusaka nambala ya foni yake. Ndinatumiza uthenga wa pafoni (SMS) yokamba zaubwenzi womwe udzathere m’banja,” adatero Ronald.

Iye adati sizidali zophweka kuti Annie avomere pempho lake chifukwa zidatenga miyezi kuti ayankhe uthengawo.

“Poti ndinafunitsitsa, ndinangoyimbano foni ndipo adati tikumane. Ine mtima udagunda kwambiri, si wokakanidwa uwu! Koma poti ndinali nditachipempherera kuti ndipeze mkaziyu, bambo, Ambuye adanditsogolera ndipo ubwenzi n’kuyamba,” adafotokoza Ronald.

Annie naye anati zinali zomuvuta akaganizira za t

sogolo la ana ake omwe bambo awo adatisiya.

“Ine ndi mayi ndiye uthengawo umafuna nthawi yokwanira kuwuunika. Sindinafune kuzunzitsa ana kaamba ka mwamuna. Koma Ronald analimbikira ndiye ndinati mwina ndi Mulungu, chofunika ndiyankhe pempho lawo,” adatero Annie.

Iye akuti sadabise mawu kukhosi oti ali ndi ana, naye Ronald adati ali ndi ake.

“Tili mkati mocheza kuchokera 2014 kufika mu December 2015 ndinaona kuti Ronald ndi bambo wokonda ana, achibale ndiponso woopa Mulungu. Kwawo kuli ana ndi zidzukulu ndi anga tiwalere limodzi motsogozedwa ndi Mulungu,” adafotokoza Annie.

Ronald ndi Annie pano akwanitsa miyezi isanu ndi umodzi ali m’banja.

Ronald amachokera m’mudzi mwa Baluwesi, T/A Makwangwala m’boma la Ntcheu. n

Related Articles

Back to top button