Chichewa

NG’AMBA IOPSEZANSO CHAKA CHINO—UNDUNA

Listen to this article

 

Chaka chatha kudali kakasi pankhani ya ulimi mvula itadula pomwe mbewu zambiri, maka chimanga, zimamasula ndipo izi zidachititsa kuti alimi ambiri asakolole mokwanira moti pano ena njala idalowa kale.

Vutoli lidagwa kaamba ka mvula ya njomba, makamaka potsatira kusintha kwa nyengo, ndipo unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi wachenjeza kuti zomwe zidaoneka chaka chatha zingathe kuchitikanso chaka chino m’madera ena.

Mlimi kudandaula ndi kufota kwa mmera m’munda chaka chatha
Mlimi kudandaula ndi kufota kwa mmera m’munda chaka chatha

Undunawu wati potengera zomwe apeza a nthambi ya zanyengo, madera ena akhoza kulandira mvula yokwana pomwe ena ayi ndipo izi zikhoza kuchititsa kuti mvula idzadule msanga m’madera ena.

Polingalira kuti alimi ambiri amadalira ulimi wa mvula, undunawu wati alimi amalize msanga kukonza minda yawo kuti mvula ikangogwa adzabzale mbewu ndi mvula yoyambirira.

“Pali chiyembekezo chakuti madera ena akhoza kulandira mvula yochepa, zomwe zingapangitse ng’amba mkati mwa nyengo ya mvulayi komanso zikhoza kupangitsa kuti mvula isiye msanga,” chidatero chikalata chomwe udatulutsa unduna wa malimidwe sabata yathayi.

Undunawu wati pofuna kuthana ndi vuto ngati lomwe lidaoneka chaka chatha mvula itadula mosayembekezera, alimi amalize kukonza minda yawo mwachangu.

Undunawu watinso alimi alingalire kubzala mbewu zocha msanga komanso atsatire njira ya kasakaniza ndi njira zamalimidwe zamakono zosunga nthaka, chinyontho ndi chonde monga kuphimbira nthaka.

Undunawu watinso pomwe ntchito zakumunda zikuyenda, alimi akangalikenso n’kukolola madzi kuti ngati mvula ingadzadule m’dera lawo, adzakhale ndi madzi okwanira a mthirira komanso omwetsa ziweto.

Polingalira za chakudya cha ziweto mtsogolo muno, undunawu wati alimi omwe ali ndi ziweto akumbukire kubzala nsenjere ndi mitundu ina ya udzu chinyezi chikakhathamira m’nthaka kuti asadzavutike nyengo ya chilimwe.

“Tikufuna alimi atsatire zimenezi kuti udindo wathu woonetsetsa kuti m’dziko muno muli chakudya chokwanira ukwaniritsidwe. Chaka chatha alimi adadzidzimutsidwa chifukwa sadayembekezere zomwe zidachitika.

“Si kuti tayamba izi chifukwa cha phunziro la chaka chatha, ayi. Tidayamba kalekale kulimbikitsa alimi kuti azikonzeka nthawi yabwino n’kumadikira mvula kuti ikangogwa azithamangira kumunda kukabzala,” adatero mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga.

Alimi ambiri adamaliza kukonza minda yawo pano koma ena akadali ndi nthitoyi ngakhale kuti m’madera ambiri mvula yagwapo kangapo kusonyeza kuti nyengoyo yayambika tsopano.n

Related Articles

Back to top button
Translate »