Chichewa

Ng’anga yochotsetsa mimba ithawa ku Mchinji

Kwa Brenda Tadi, sing’anga Nasikiti udali ulalo wochotsera pathupi kufuna kuzemba uchembere omwe tate wake sakudziwika koma mapeto ake watsikira kuli chete.

Sing’angayo atazindikira kuti mankhwalawo agwira ntchito molakwika adasamuka mwachinsinsi ndipo mpaka pano anthu a mmudzimo ndi apolisi sakudziwa komwe adalowera.

Wojambula watu akuona ngati zidali choncho patsikulo
Wojambula watu akuona ngati zidali choncho patsikulo

Msungwanayu yemwe adali ndi zaka 20 adazindikira kuti ali ndi pathupi pa miyezi itatu ali kale ndi mwana wina wa chaka chimodzio ndipo sadali pabanja.

Mneneri wa polisi ya pa Mchinji Moses Nyirenda adatsimikiza za imfa ya Tadi ndipo adati wachinansi wake, Chifundo White, adauza apolisiwo kuti Tadi adakwatiwapo koma banja lidatha ndipo amangokhala pankhomo pamakolo ake.

White adati pa 11 October, 2015 Tadi atazindikira za mimbayo adapita kwa sing’anga Nasikiti yemwe adamupatsa mankhwala azitsamba nkumuuza kuti akamwe kuti mimbayo ikachoke koma zinthu zidatembenuka.

“Atamwa mankhwalawo, pa 12 [October 2015] adayamba kudandaula mmimba momwe amagudubuka namo nkumabuula ngati mwana. Titamufunsa adaulula kuti adakatenga mankhwala ochotsera mimba kwa sing’anga Nasikiti,” adatero White.

Iye adati sing’angayo adali wodziwika kuderalo koma sadamvekeko mbiri yopereka mankhwala omwe zotsatira zake zidali zomvetsa chisoni ngati imfa ya mnasi wake, Tadi.

White adati Tadi adamwalira pa 13 October 2015 vuto la mmimbalo litafika posautsa kwambiri ndipo azitsamba ena atalephera kukonza zinthu.

Nyirenda adati za imfa ya msungwanayo zitamveka, anthu adali balalabalala kumusakasaka koma sadamupeze ndipo apolisi atafika kusakako kudapitirira komabe popanda chooneka.

Iye adati sing’angayo akadzapezeka adzazengedwa mlandu wopereka mankhwala oipa kwa munthu komanso kuchotsa pathupi zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino.

Tadi amachokera m’mudzi mwa Nkhumba T/A Mavwere m’boma la Mchinji.

kuderalo koma sadamvekeko mbiri yopereka mankhwala omwe zotsatira zake zidali zomvetsa chisoni ngati imfa ya mnasi wake, Tadi.
White adati Tadi adamwalira pa 13 October 2015 vuto la mmimbalo litafika posautsa kwambiri ndipo azitsamba ena atalephera kukonza zinthu.
Nyirenda adati za imfa ya msungwanayo zitamveka, anthu adali balalabalala kumusakasaka koma sadamupeze ndipo apolisi atafika kusakako kudapitirira komabe popanda chooneka.
Iye adati sing’angayo akadzapezeka adzazengedwa mlandu wopereka mankhwala oipa kwa munthu komanso kuchotsa pathupi zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino.
Tadi amachokera m’mudzi mwa Nkhumba T/A Mavwere m’boma la Mchinji.

Related Articles

Back to top button