Chichewa

‘Ngozi idazamitsa chikondi chathu’

Listen to this article

Anthu adavulala, ena adataya miyoyo yawo. Koma kwa Joseph Chirwa ndi Towera udali mwayi kuti awiriwa akumane ndi kumanga woyera.

Lero ndi thupi limodzi, koma nkhani yano imaseketsabe akakumbuka za ngozi yomwe idachitika mu 2010 m’boma la Zomba, iyo idali ngozi ya basi.

Towera adali m’basimo ndipo adavulala ndi kutengeredwa kuchipatala. Panthawiyo n’kuti awiriwa atakumana kale ndi kupatsana manambala koma zolota kuti akapizana mawu a chikondi panalibe.

Joseph ndi Towera lero ndi banja

Joseph yemwe akugwira ntchito kunthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno atamva kuti Towera wapanga ngozi, adakhudzidwa ndipo samati waimbanso liti foni komanso kukamuona.

“Chifukwa choimbaimba, tidakhala pachinzake kwambiri, kenaka tidayamba kufunana,” adatero Joseph pamene adamudikira Towera achire kaye kuti nkhani yachikondi ilowe m’bwalo.

Joseph akuti pamene izi zimachitika n’kuti awiriwa atakumana kale ku Masintha CCAP komwe onsewa amapemphera.

Apo Joseph n’kuti ali mtsogoleri wa achinyamata, Towera adali membala wagulu la maimbidwe.

Komabe panthawiyo zoti angadzakhale thupi limodzi sizimadziwika. Zidatengera ngozi ya ku Zomba kuti zenizeni zioneke.

Mu 2012 Towera adali atachita, ndipo Joseph adaponya Chichewa. Pounguza chikondi chomwe mtsogoleriyu adachionetsa pa nthawi ya matenda, Towera sadazengereze koma kuvomera.

“Joseph ndi oopa Mulungu. Wachikondi komaso wosamala. Iye amalingalira mwakuya ndipo ndidapeza tsogolo langwiro mwa iye,” adatero Towera.

Naye Joseph adabwekera kuopa Mulungu kwa njoleyo: “Towera ndi oopa Mulungu, ali ndi maonekedwe abwino ndipo ndisanamepo mkazi wanga ndi nthwani.”

Ukwati udali pa 31 October 2015 ku Masintha CCAP ndipo madyerero adali ku ku Lilongwe Golf club.

Tikukambamu, awiriwa ali m’dziko la India komwe akuchita maphunziro a Master in Business Administration (MBA). n

Related Articles

Back to top button
Translate »