Nkhani

Nigeria, Malawi agwilana manja

Listen to this article

Pamene dziko la Malawi lili mkati mwazokambirana ndi dziko la Tanzania pa nkhani ya umwini wa nyanja ya Malawi yomwe akuti muli mafuta, dziko la Nigeria lati ndilokonzeka kuthandiza dziko lino kuwenga mafutawa.

Mtsogoleri wa dziko la Nigeria Goodluck Jonathan adanena izi Lolemba pamene amafika m’dziko muno kudzacheza kwa masiku awiri motsagana ndi akuluakulu ena 143 ochokera ku Nigeria komweko.

Dziko la Nigeria ndilimodzi mwa mayiko omwe amawenga mafuta ambiri pa dziko lapansi ndipo Jonathan adati dziko lawo ndilokonzeka kutumiza akatswiri antchito zowenga mafuta kuchokera kudziko lawo kuti adzathandize ntchito zowenga mafuta mu nyanja ya Malawi.

“Dziko la Nigeria lakhala likuwenga mafuta kwa zaka zambiri ndipo padakali pano tili ndi akatswiri odziwa bwino za ntchito yowenga mafuta omwe tikhoza kuwatumiza kuti adzathandize pa ntchito yotere kuno,” adatero Jonathan.

Related Articles

Back to top button
Translate »