Nkhani

Njala ikhaulitsa a Malawi

…Ma Admarc ena kuli gwagwagwa!

Zafika pena. Ngati wina samwalira ndi njala ungokhala mwayi chabe koma zinthu zaipa m’dziko muno moti anthu ena akugona kumimba kuli pululu.

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akunenetsa kuti palibe amene amwalire ndi njala, koma ngati sipachitika china chake m’misika ya Admarc m’dziko muno ena amwalira nayo.

Mzere wa ofuna kugula chimanga ku Admarc
Mzere wa ofuna kugula chimanga ku Admarc

Ulendo wa Tamvani m’maboma a chigawo cha kummwera, pakati komanso kumpoto, wapeza kuti madera ena patha miyezi ingapo chimanga chikusowa m’misika ya Admarc.

Ma Admarc a Chikomwe, Ngwerero, Nasawa, Mayaka, Sunuzi, Jenala, Zaone ndi Buleya m’boma la Zomba kwa T/A M’biza akuti atha miyezi iwiri kulibe chimanga.

Gulupu Belo wati malinga ndi kusowa kwa chimangacho, anthu amagonera deya amene amagula pamtengo wa K240 pa kilogalamu.

“Panopa amene wapeza gaga ndi munthu. Chakudya chasowa, moti ndatumiza anthu 8 kuchipatala amene amaonetsa zizindikiro zachilendo chifukwa chosadya,” adatero Belo.

Ku Mwanza malinga ndi T/A Kanduku, miyezi iwiri yatha chimanga kulibe. Iye wati poyamba anthu amagonera mango koma lero ndiye kolowera kwasowa.

“Ndi nkhani yosabisa, njala yavuta kuno ndipo chimanga chatenga nthawi chisadafike ku Admarc,” adatero Kanduku.

Ku Balaka patha miyezi iwiri chimanga chisadafike pa Admarc ya Phalula pamene kwa Sosola ndiye patha mwezi.

Sabata yatha tidapeza anthu am’mudzimo akupita kukadandaula kwa DC wa bomalo chifukwa akhala akuuzidwa kuti chimanga chibwera koma kuli chuuu.

Admarc ya Misuku ku Chitipa ikumalandira chimanga mwezi ulionse kamodzi koma chimangacho chikuchokera kubungwe la World Vision. Admarc ya Chikwera m’bomalo ilibiletu chimanga, pamene Admarc ya paboma yangolandira kumene matumba 300. Mabanja 2 000 ndiwo amadalira Admarc ya pabomayo koma ikugulitsa makilogalamu osaposa 15 kwa aliyense.

Admarc ya pa Karonga boma ili ndi chimanga koma pamene timafikapo Lachiwiri m’sabatayi n’kuti pali mnzere wotalika ndi mamita 280. Anthu akumagona pomwepo kuti agule chimanga.

Ma Admarc a boma la Nkhata Bay akuti akumalandira chimanga pafupipafupi koma chikumatha tsiku lomwelo chifukwa chikumafika chochepa kuyerekeza ndi anthu amene akufuna chakudyacho.

Mkulu wa bungwe la Admarc Foster Mulumbe wati chiyambireni September chaka chatha agulitsa matani 26 000 a chimanga. Iye watinso kufika pano, Admarc yatsala ndi matani ochepa.

“Chimanga chidakalipo koma chochepera, ndipo tikupitiriza kupereka m’misika yathu. Ngati chimanga chatha m’misika yathu, ndi bwino kutidziwitsa msanga kuti titumize china,” adatero Mulumbe.

Miyezi ingapo yapitayo, boma lidagula matani 30 000 a chimanga m’dziko la Zambia.

Woyendetsa ntchito wamkulu mu unduna wa malimidwe Bright Kumwembe wati chimanga chonsecho chidapita kumisika ya Admarc.

“Chimanga chonsecho chidafika m’dziko muno ndipo chili m’misika ya Admarc. Likulu losamala chakudya la National Food Reserve Ageency [NFRA] likugula chimanga china m’dziko momwe muno,” adetro Kumwembe.

Nkhani ya njala si yachilendonso m’dziko muno. Bungwe la World Food Programme (WFP) lati lakwanitsa kufikira anthu 1.6 miliyoni m’maboma 15 amene ali pamoto wa njala.

WFP Lolemba lidatulutsanso lipoti lina lomwe limati anthu 14 miliyoni ali pachiopsezo chokukutika ndi njala kummawa kwa Africa.

Dziko la Malawi ndi limodzi mwa maiko okhudzidwa chifukwa cha mavuto a kusowa kwa mvula.

 

Related Articles

Back to top button