Nkhani

Njala yafikapo, ena akugonera mango

Listen to this article

Pali chiopsezo kuti anthu ena angafe ndi njala yomwe yagwa m’madera awo.

Anthuwa ati ngakhale boma likugawa chimanga m’maboma omwe akhudzidwa, chimangachi ati ndichochepa kuyerekeza anthu omwe akhudzidwa pomwe ena akuti sadalandirebe chimangachi ngakhale madera awo njala yafika posauzana.

Maderawa ndi monga Neno, Dedza, Mwanza, Chiradzulu, komwe anthu akugonera mipama ndi mango.

Mayi Esther Chibwana wa m’mudzi mwa Mithiko kwa T/A Mpama m’boma la Chiradzulu ali ndi ana anayi ndipo amuna ake sagwira ntchito.

Mayiyu wati adakolola matumba atatu achimanga koma chimangacho chidatha mu Julaye.

Apa moyo udayamba kulimba pomwe adayamba kukhalira maganyu ndipo akadya bwino ndiye kuti agonera gaga yemwe walimitsa.

“Timalowa m’taunimu [Chiradzulu boma] komwe timapeza maganyu olima m’munda ndipo timalimitsa gaga koma pano gagayonso akusowa ndiye tikumalimitsa mango omwe tikumakagonera.

“Ngati sitipeza chakudya ndiye timagonera mango apo ayi kukangogona koma ndi ana kumakhala kovuta,” watero mayiyo, yemwe ndi wa zaka 30 ndipo akuti chimanga ngakhale ufa sizidagawidwe kumeneko.

Iye wati kumudziko mavuto akusowa kwa chakudya afikapo ndipo chiyembekezo chotaya miyoyo chakula.

Nyakwawa Benito ya kwa T/A Mlauli m’boma la Neno yati anthu 290 ndiwo akufunika thandizo lachimanga koma mudzi wake udalandira matumba 100.

“Tangogawana ndipo ena amapita ndi makilogalamu atatu nanga tikadatani?” watero Benito.

Naye Gulupu Mlauli wati mwa anthu 360 omwe akufuna thandizo, mudziwo walandira matumba 110 zomwe zayika ena pamavuto.

“Anthu onse adzagwada kwa ine kufuna thandizo chifukwa njala yagwira aliyense kuno chifukwa sitidakolole kaamba ka vuto la mvula,” watero Mlauli.

T/A Kachindamoto ya m’boma la Dedza yati anthu 70 000 ndiwo akufunika thandizo koma kumeneko adalandira matumba 500 achimanga.

“Pena ukuchita kukanika kutuluka m’nyumba kuopa anthu chifukwa akuwona ngati vuto ndi ine. Tithokoze boma chifukwa talidandaulira za vutoli ndipo chiyembekezo chilipo kuti litithandizanso,” watero Kachindamoto.

T/A Nthache ya m’boma la Mwanza yati kumeneko chimanga sichidafike ndipo sakudziwa kuti chifika liti.

Iye wati anthu kumeneko akugonera mango pomwe ena mipama kaamba ka njalayi.

Mfumuyi yati pa 17 Novembala chaka chino mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda adakapereka ufa koma amagawa matumba 10 m’mudzi uliwonse.

“Pano zinthu zikupitirira kuvuta, miyoyo ya anthu ili pamoto. Kuno ku Mwanza njala ikukhudza aliyense chifukwa palibe yemwe adakolola.

“Chonde boma litikumbuke ndi chimanga chomwe anzathu akulandira,” adatero Nthache yemwe adati thandizo likachedwa anthu atha kutaya miyoyo.

Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu wati sakudziwa kuti m’madera ena mudafika chimanga chosakwana kotero ayambe wafufuza kaye.

“Sindikudziwa kuti zili choncho komabe ndifufuza. Ku Dedza mukunenako ndikadzimvera ndeka chifukwa lero [pa 21 Novembala] ndikupita komweko.

“Komabe ndithokoze kuti anthu akubwera poyera ndikunena zomwe akukumana nazo ndipo izi zitithandiza,” adatero Kunkuyu.

Ngakhale malipoti amawonetsa kuti chaka chino tili ndi chakudya choposera pa mlingo wake komabe njala yatenga malo.

Pulezidenti wa dziko lino adavomereza kuti ngakhale malipoti amasonyeza kuti anthu oposa 1.7 miliyoni ndiwo akhudzidwe ndi njala koma chiwerengerochi chitha kuposa pa 2 miliyoni.

Related Articles

Back to top button
Translate »