Nkhanza zanyanya

Listen to this article

Bambo wina wa zaka 31, walaula dziko pomwe akumunazira kugwiririra khanda lalikazi la miyezi 5. Pakadali pano Muderanji Kanjira ali m’manja mwa apolisi.

Nkhaniyitu idatuluka Lachitatu pa 25 November pomwe anthu adali pa kalikiliki ndi zochitika zoyamba  masiku 16 olimbana ndi nkhanza za m’banja.

Malinga ndi mneneri wa polisi ya Zomba Patricia Sipiliano, Kanjira adapempha makolo a khandalo kuti akacheze nalo chifukwa ngoyandikana nyumba.

Mbuyomu, atolankhani aakazi adachita zionetsero zokwiya ndi kugwiririra

“Patadutsa ola limodzi adakalibwenza khandalo koma likulira kwambiri ndipo mayi ake pomusintha adaona magazi pa zovala zake komanso mabala kumalo ake obisika,” adalongosola Sipiliano.

Iye adati ngakhale zotsatira zochokera kuchipatala chachikulu cha Zomba zatsimikiza kuti khandalo lidagwiriridwa.

Kanjira amachokera m’mudzi mwa Mtiya,  kwa T/A Mlumbe m’boma la Zomba.

Ndipo kumapeto a sabata yatha, kudatuluka uthenga wa mwana wina ku Chigumula amene adatepa bamboo ake pomwe amamunyengerera kuti akagone nawo. Bamboyo amakakamira mwanayo kuti akagone naye posinthanitsa ndi fizi.

Malinga ndi zomwe mwanayu watumiza m’masamba a mchezo, bamboyo yemwe sakudziwika bwino dzina lake akumveka akumuuza mwanayo kuti akavulire zonse pabalaza ndipo akalowe kuchipinda kwa bamboyo ali maliseche ngati chibalo chokana kugona naye mmbuyomu.

“Ndidaganiza zowajambula palamya akukamba zawozo chifukwa nthawi zambiri n’kamadandaula anthu amandinena kuti ndine wabodza,” adatero mtsikanayo.

Izi zili apo, m’boma la Dowa, apolisi atsekera mnyamata wina wa zaka 21 yemwe adagwiririra ana amuna anayi a zaka kuyambira 10 mpaka 17 ndi kuwapatsanso matenda opatsirana pogonana.

Malinga ndi mneneri wa apolisi m’boma la Dowa, Gladson M’bumpha, Innocent Poita akuganiziridwa kuti wakhala akugwiririra anawa kuchoka m’chaka cha 2016 kufika pa 19 November chaka chino m’mudzi wina ku Dowako.

“Anyamatawa amapita kunyumba kwake kukaonera kanema pa lamya yake ya m’manja.  Ndipo pa 19, atamaliza kuonera kanemayo, mmodzi mwa anyamatawo adatsalira kunyumbako zomwe zidapangitsa anzakewo kukaulula kwa makolo ake kuti Poita amawagona akakhala kunyumba kwake,” adalongosola M’bumpha.

Poti amachokera m’mudzi mwa Ndalama kwa T/A Chiwere, m’boma la Dowa.

N’zodandaulitsa kuti pomwe mbali zina zili pa likiliki kuyesetsa kuthana ndi mchitidwe wogwiririra zinthu zikunka zikipiratu.

M’chaka cha 2018, apolisi adapeza kuti ana 1 539 ndiwo adagwiriridwa, pomwe m’chaka cha 2019 anthu 1 766 adagwiriridwa ndipo kuchoka January chaka chino kufika mwezi wa September ana 1 501 adagwiriridwa.

Izi zikutanthauza kuti  pofika mwezi wa mawa wa December chiwerengerochi chikhala chitadutsa chiwerengero cha chaka chatha cha 1 766.

Komatu si ana okha omwe akukumana ndi nkhanza m’dziko muno chifukwa ngakhale nawo atsikana komanso amayi akukumana nazo.

Pomwe Msangulutso udacheza ndi amayi ena omwe amagwira ntchito yoyendayenda mumzinda wa Mzuzu, zidaululikanso kuti amayiwa amagwiriridwa makamaka ndi abambo ogwira ntchito za chitetezo monga apolisi ndi asilikali.

Mmodzi mwa amayiwa yemwe sitimutchula dzina pomuteteza adati ambiri mwa abambo azachitetezowa amawagona ulele powaopseza komanso akamaliza pamenepo amawamenya.

“Sabata yomwe ino, bambo wina wa chitetezo adandigona mondikakamiza komanso sadagwiritse ntchito chitetezo. Atatha pamenepo adandimenya komanso kunditengera zakudya ndi zakumwa zomwe ndidali nazo,” iye adalongosola.

Polankhulapo pa nkhanza zomwe zikuchitikira amayi, atsikana ndi ana a m’dziko muno, Jessie Ching’oma wochokera ku bungwe lomwe si laboma la NGO Gender Coordinating Network (NGO-GCN) adati anthuwa akufunika zilango zokhwimitsitsa, zoopsa kuti ena atengerepo phunziro.

“Anthuwa akufunika zilango zomwe sizidalembedwe, zilango zoopsa kuti mwina mchitidwewo uchepeko,” adalongosola Ching’oma.

Pomwe Amos Nyaka yemwe amamenyeranso ufulu adauza msonkhano wa achinyamata mumzinda wa Mzuzu kuti mpofunika kuunikanso zina mwa zikhalidwe zathu chifukwa ndi zomwe zikupititsa patsogolo mchitidwewu.

Related Articles

Back to top button
Translate »