Nkhani

 Nkhawa ikulirakulira pankhani ya zaumoyo

Listen to this article

Mabungwe omwe si aboma ati mavuto a mgonagona omwe akuoneka pa nkhani za umoyo m’dziko muno ndi umboni wakuti chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) sichikukwaniritsa zomwe chidalonjeza pomwe chinkachita misonkhano yokopa anthu kuti achivotere pachisankho cha chaka chatha.

Kuperewera kwa ogwira ntchito zaumoyo, kusowa kwa mankhwala, kusowa kwa chakudya ndi ganizo la boma lochepetsa chakudya chomwe limapereka kwa odwala m’zipatala ndi ena mwa mavuto omwe mabungwewa ati akula padakalipano.

Anamwino kukapereka madandaulo awo ku Nyumba ya Malamulo
Anamwino kukapereka madandaulo awo ku Nyumba ya Malamulo

Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu pa nkhani za umoyo, Charles Nyirenda, wati zomwe boma likupanga pochita zinthu “modzidzimukira” ndi msampha waukulu pa miyoyo ya anthu.

Nyirenda ndi mmodzi mwa oimira mabungwe amene athirapo ndemanga pa zomwe zikuchitika m’dziko muno, makamaka pankhani ya za umoyo wa anthu womwe uli pachiswe chifukwa cha mikwingwirima yomwe unduna wa za umoyo akukumana nayo.

Iye adati mmene zinthu zikuyendera pankhani za umoyo, tsogolo lenileni silikuwoneka ndipo kukadakhala bwino boma likadangopanga mfundo imodzi n’kuikhazikitsa osati kuvinavina.

“Poyamba nkhani imene idavuta ndi yakuti anthu azilipira m’zipatala yomwe idatsutsidwa mpaka kuzilala. Pano akuti anthu odwala azidya kamodzi patsiku komanso mankhwala m’zipatala sakupezeka. Anthu akumawauza kuti akagule okha, tsono apa zikusiyana pati n’kulipira kuchipatala?” adatero Nyirenda.

Iye adati chidali chanzeru kuyamba kulipiritsako bola anthu ovutika, koma odwala azidya chakudya chokwanira kuti mankhwala azigwira ntchito m’thupi.

Mmodzi mwa omenyera maufulu a anthu m’dziko muno, Gift Trapence, adati boma likuyenera kuyankhapo pa nkhawa zomwe anthu, kudzera kumabungwe, akupereka m’dziko muno chifukwa lidawalonjeza kukonza mavuto amene akukumana nawowo.

“Apa ndi nkhani yoti boma lichitepo kanthu msanga chifukwa lidalonjeza lokha anthu asadalisankhe ndiye zisakhale ngati anthu akupempha ayi koma akungokumbutsa zomwe adalonjezededwa,” adatero Trapence.

Mavutowatu akudza patangotha pafupifupi chaka ndi miyezi 6 kuchoka pomwe chipani cha DPP chidayamba kulamula chitapambana pachisankho cha mwezi wa May, 2014.

Chisankho chisadachitike, chipanicho chidalonjeza kuti chidzatukula nkhani zaumoyo poonetsetsa kuti chiwerengero cha anthu ogwira ntchito zaumoyo ndi chokwanira, mankhwala akupezeka m’zipatala, kutukula moyo wa anthu ogwira ntchito zachipatala ndi kuchepetsa imfa zokhudza uchembere.

Malonjezowo ali choncho, boma lidaplephera kulemba ntchito madotolo 51 amene adamaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine, chonsecho ngakhale bungwe la zaumoyo padziko lino la World Health Organisation (WHO) limati madotolo 23 alionse ayenera kuthandiza anthu 10 000, ku Malawi, madotolo awiri amathandiza odwala 100 000.

Ndipo posachedwa, Amalawi zikwizikwi m’boma la Rumphi adayenda ulendo wokapereka madandaulo kwa DC wa m’bomalo pokhudzidwa kuti odwala akulandira chakudya kamodzi patsiku pomwe akumwa mankhwala ofunika chakudya chokwanira.

Ulendo wokapereka zodandaula za chakudya udakonzedwa ndi mgwirizano wa mabungwe omwe si aboma m’bomalo ndipo wapampando wa mgwirizanowo, Eunice Banda, adati zomwe

zikuchitikazi zikusonyeza kuti boma likulephera kukwaniritsa lonjezo.

“Kutengera zomwe adalonjeza a Pulezidenti kuti sadzalola munthu aliyense kumwalira ndi njala, tikuona kuti zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kulephera kukwaniritsa lonjezolo,” adatero Banda.

Iye adati si zoona kuti munthu yemwe akulandira mankhwala aziperewera chakudya m’thupi mwake chifukwa mankhwala amagwira bwino ntchito ndi chakudya.

Komanso poona kuti sizikuwayendera pantchito yawo, anamwino ena adakaperekanso chikalata chawo ku Nyumba ya Malamulo pozizwa ndi ganizo la boma lakuti anamwino ena amene adalembedwa kale ntchito akayesedwenso.

M’chikalata chawo, anamwinowo adadandaula za momwe ntchito za umoyo zalowera pansi m’dziko muno ndi momwe umoyo wa Amalawi wakhudzidwira, zomwe adati gwero lake ndi kusalingalira nkhani za umoyo pakati pa atsogoleri.

M’chikalatachi, adatinso ndi okhudzidwa kuti boma likulephera kulemba madotolo ndi anamwino omwe adamaliza maphunziro awo chonsecho ogwira ntchito zachipatala ndi ochepa, zomwe zimachititsa kuti ntchito yawo iziwawa.

Koma nduna ya zachuma ndi chitukuko, Goodall Gondwe, ati pali mpumulo kumbali nkhani ya chiwerengero cha madotolo ndi anamwino chifukwa maiko omwe amathandiza dziko lino avomereza kuti boma likhoza kugwiritsa ntchito ndalama zina zomwe zidali za ntchito yolimbana ndi malungo, chifuwa chachikulu ndi matenda a Edzi polemba ntchito madotolo ndi anamwino omwe lidalephera kuwalemba.

Gondwe adati ndalamazi zikhoza kukwana kulipira anthuwa kwa chaka chathunthu ndipo maiko othandizawo ati boma liwonetsetse kuti zikadzatha ndalamazi, lidzapeze ndalama zopitirizira kulipira anthuwa. n

Related Articles

Back to top button