Chichewa

Nkhoma yakhumudwitsa DPP, UTM

Listen to this article

Zipani za Democratic Progressive Party (DPP) ndi UTM zati zakhumudwa ndi kalata yomwe Sinodi ya Nkhoma ya mpingo wa CCAP yatulutsa sabata yatha.

Kalatayo, yomwe siidatchule dzina la mtsogoleri aliyense, ikufotokozera Akhristu ampingowo munthu woyenera kudzamuvotera.

Kaliati: Nkhoma yalakwa

Kalatayo ikuti mtsogoleri woyenera kumuvotera ndi yemwe ali wodzadzidwa ndi Mzimu Woyera, wangwiro, wokonda chitukuko, wosasankha anthu potengera mitundu yawo, komanso yemwe ali ndi chidwi chothana ndi katangale.

Nduna yofalitsa nkhani, Henry Mussa, adati mpingowo usaiwale kuti mmbuyomu nawonso udakhudzidwa ndi nkhani za ziphuphu ndi katangale.

M’chaka cha 2014 ena mwa ogwira ntchito ku Sinodi ya Nkhoma adanyambita K61 886 389.11 ya ntchito zachitukuko.

Boma la America ndilo lidapereka ndalamazo kudzera bungwe lake la chitukuko la United States Agency for International Development (USAaid).

Mlembi wa Nkhoma pa nthawiyo, mbusa Vasco Kachipapa, adavomera kuti zinthu zidalakwika ndipo Sinodiyo idabweza ndalamazo.

“Membala wa mpingo kapena chipembedzo chilichonse chili ndi ufulu wopikitsana nawo pa mpando uliwonse wa ndale. Choncho n’kulakwa kuti mpingo uzisiyanitsa anthu kuti ena ndiwoyera kuposa anzawo,” kalata yomwe boma latulutsa ndipo yasayinidwa ndi Mussa yatero.

Ndunayi idati mfundo za Sinodiyo zangokolanakolana m’kalatayo.

Naye mlembi wa UTM, Patricia Kaliati, adati zomwe yachita Sinodiyo pouza mamembala ake kuti atsogoleri ena ndi woyera poyerekeza ndi anzawo n’kulakwa, komanso n’zogawanitsa anthu.

“Tikayamba kufukulana, kodi pakhala zabwino? Mtsogoleri aliyense kuti tiyambe kumuunika mbiri yake, kodi woyera mtima apezekapo ngati momwe ikulankhulira Sinodiyo? Zinazi tiyeni tiziweruza ndi mtima wangwiro,” adatero Kaliati.

Iye adati Sinodi ngati mpingo idayenera kuuza nkhosa zake kuti zisafooke m’mapemphero, kupembedzera dziko lino kuti zisankho zidzayende bwino osati kubzala mbewu zamipatuko mitima mwawo.

M’kalata yake Sinodi ikuti boma silikuonetsa chidwi pofufuza kuphedwa kwa mnyamata wa ku Polytechnic Robert Chasowa, mmodzi mwa akuluakulu a Anti-Corruption Bureau (ACB) Issa Njauju ndi Buleya Lule yemwe amakhudzidwa ndi nkhani yodzembetsa mwana wachialubino.

Mbusa wamkulu mu Sinodiyo, mbusa Bizwick Nkhoma, adati mpingo wake umalembera Akhristu ake kalatayo osati chipani chilichonse. Choncho sangayankhe pa zomwe anthu kapena chipani chilichonse chikulankhula.

Related Articles

Back to top button
Translate »