Chichewa

Nkhondo ya mkalabongo ikadali mkati

Nthambi yoyeza katundu pamsika ya Malawi Bureau of Standards (MBS) yati nkhondo yothana ndi mkalabongo ikuyenda bwino chifukwa opanga mowawu avomereza kuti samatsata malamulo a dziko lino.

Mkulu wa MBS, Davlin Chokazinga, adanena izi pothirira ndemanga pa ganizo la bungwe la Alcohol Manufacturers Association (AMA) lochotsa pamsika mkalabongo pofuna kuchita malonda moyenera.

Chokazinga adati kampanizi zathinidwa chifukwa ku khothi komwe amadalira zazindikirika kuti mowawu siwothandiza Amalawi.

mkalabongo

“Mkalabongo siwovomerezeka m’dziko muno. Kampanizi zakhala zikutenga ziletso kukhoti tikalimbikitsa ntchito yothana ndi mowawu pamsika. Ngakhale timalanda masatifikite ndi kutseka malo, amapangabe moderera,” adatero Chokazinga.

Iye adati akhala akuletsa mowawu chifukwa mphamvu yake ndi yochuluka kwambiri yomwe imaika miyoyo ya anthu pa chiswe komanso uli m’mabotolo osavomerezeka (pulasitiki).

“Opangawa samwanso mowawu ndipo sungagulitsidwe kunja. Amaphwanya lamulo 210 la  Malawi Standards. Mabotolo alibenso chizindikiro cha MBS kusonyeza kuti amachita opanda upangiri wathu. Mwadongosolo lake akuyenera kuika m’mabotolo a galasi komanso tiziwapatsa mlingo wamphamvu oyenera kuti omwa asavulale monga zikuchitikiramu,” iye adatero.

M’chikalata chomwe chasayinidwa ndi wapampando wa bungwe la kampanizi Raj Munnangi Lolemba, chapempha anthu kubwenza mowawu chifukwa sukukwaniritsa ngodya za MBS komanso sioyenera kuti munthu azimwa.

Munnangi adati nthumwi zotolerera mowawu zatumizidwa m’zigawo zonse m’dziko muno ndipo anthu azibwenzeredwa ndalama zawo.

“Iyi ndi njira yokwaniritsa khumbo lathu lopereka zinthu zoyenera kwa Amalawi. Kampani iliyonse isindikiza uthenga woyitanitsa mowa wake,” adatero Munnangi.

Iye adati pomwe akulimbikitsa kampani zawo kutsatira malamulo, MBS ionetsetse kuti aliyense pamsika akuchita chimodzimodzi chifukwa ena sali pansi pawo.

“Palinso mowa wambiri pamsika omwe uli m’mabotolo a pulasitiki zomwe zikhonza kusokoneza malonda athu pomwe tikutsatira malamulo,” adatero Munnangi.

Mkulu wa bungwe la Drug Fight Malawi, Nelson Zakeyu, yemwe wakhala akutsutsa kupezeka kwa mkalabongo pamsika, adati nthawi yakwana yoti boma likhwimitse lamulo lokhudza mowa lomwe lidavomerezedwa pa 26 January chaka chino.

“Kampanizi zakonzeka kuthandiza dziko kukwaniritsa mfundo yachitatu ya chitukuko ya United Nations (UN) gawo 3 ndime 3.5 yolimbikitsa umoyo wabwino pothana ndi uchidakwa, kusuta fodya ndi zina. Ukali wa mowawu ukhala oyenera chifukwa MBS izigwira ntchito yake kusiyana ndi mlingo womwe ukulumalitsa ubongo, mapapo ndi impso komanso nkhope za anthu,” adatero Zakeyu.

Mwa mowa omwe kampanizi zikupempha kuti anthu abwenze ndi monga Super Midori, XXX Rum, Chikoka, Black Ponda Rum, Leader and Striker, Win Vodka ndi Rejoice. n

Related Articles

Back to top button