Chichewa

Nkhukutembo ndi dilu

Amaweta nkhukutembo mofanana ndi nkhuku pozipatsa madeya ndi ndiwo zamasamba komanso madzi. Makola nawo ndi osasiyana ndipo zimatha kugonera m’khola limodzi.

Koma mlimiyo, Eddie Mlenga wa ku Chilomoni mumzinda wa Blantyre akuti pa zifuyo ziwirizi, nkhukutembo imatsogola chaka chikamatha.

Iwo adati izi zili choncho chifukwa pakutha pa chaka nkhukutembo imakhala yakula kwambiri choncho kuphatikiza ndi kukoma kwa nyama yake mtengo umakhala kutalitali kwambiri ndi nkhuku.

“Nkhukutembo yaimuna ikafikapo ndimagulitsa mtengo wosachepera K25 000 imodzi chifukwa imatha kumalemera makilogalamu 15 kupita m’mwamba pamene nkhuku singagulitsiddwe ngakhale pa mtengo wa K10 000.

Muli makwacha mu ulimi wa nkhukutembo

“Misika yake nayo sindisowa chifukwa anthu tsopano azindikira kuti ndi nyama yokoma choncho amadzandigula pakhomo,” iye adatero.

Mkulu wa nthambi ya zaulangizi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) a Jonathan Tanganyika adati kusiyana ndi nkhuku, ulimi wa nkhukutembo sulowa pansi ndi matenda osakaza a chitopa.

Iwo adati izi zili chomwecho chifukwa ngakhale matendawa agwe kudera, zifuyozi zimangonyamula matendawa koma osadwala nawo choncho zimapulumuka.

“Kudyetsera ziwetozi sikusiyana ndi ndondomeko ya mmene mlimi angadyetselele nkhuku koma chimasiyana ndi kuchuluka kwa mchere wa pulotini m’chakudyacho.

“Mwachitsanzo, anapiye akangogogomoledwa amayenera kupatsidwa chakudya choyambiririra chotchedwa starter ndipo mcherewu ukuyenera utenge magawo 28 pa 100 aliwonse kuti anyamuke ndi thanzi lokwanira,” iye adatero.

Mkuluyu adafotokoza kuti anapiyewa amayenera kuumirizidwa kuyamba kudya chakudyachi m’maola 36 oyambirira chifukwa mlimi akachedwetsa amavutika kudya.

Iwo adati anapiye amayenera kusungidwa m’khola lotentha bwino lija limadziwika kuti brooder m’Chingerezi kufikira atakulirapo kuti asafe ndi kuzizira ndipo mlimi awadule milomo kuopetsa kuvulazana mtsogolo.

Kuyambira sabata zinayi mpaka 8 Tanganyika adati kuchuluka kwa chakudya chokulitsa kukuyenera kutsika ndi magawo awiri pa 100 aliwonse.

“Akakwanitsa sabata 8 kapena 10 akhoza kumawetedwa ngati zazikulu mu khola momwemo ndi kumazipatsira chakudya cha kasakaniza ndi za masamba kuti zikule msanga kapena kumazitulutsa kuti zizikadyakonso za m’gulu la udzu.

“Kudyetsera panja kumathandiza kuchepetsa ndalama yolowa ku chakudya,” iwo adtaero.

Malingana ndi mkuluyu, khola la nkhukutembo limayenera likhale lolimba bwino pansi, louma, la malo okwanira, laukhondo, losadontha ndi lolowa mpweya bwino kuti mlimi apewe matenda.

Ngakhale nkhukutembo sizifa ndi matenda a chitopa ngati nkhuku, a Tanganyika adati zimavutika ndi matenda ena ndi tizirombo.

Iwo adati utitiri umavuta kwambiri ziwetozi choncho pamafunika kuonetsetsa m’khola kapena malo amene zimabisala kuti ngati muli utitili mlimi apopere kapena kuwazamo mankhwala kuti ufe.

“Kulekerera utitiri ndi koopsa chifukwa umayamwa magazi ndi kufalitsa matenda,” adafotokoza motero.

Wothandizira kafukufuku wa ziweto ku nthambi ya zakafukufuku wa zaulimi kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo Mphatso Sumani adaonjeza kuti ulimiwu ndi wabwino chifukwa kafukufuku adapeza kuti nyama ya nkhukutembo imakhala ndi mafuta ochepa ndipo magawo 70 pa 100 aliwonse a nyama yake imakhala yoyera.

Related Articles

Back to top button