Chichewa

Ntchito ilipo

Listen to this article

 

Zilikoliko mawa lino kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium kumene mphunzitsi wa timu ya dziko lino Ernest Mtawali akuyembekezeka kutsogolera anyamata ake kuchita chamuna chogonjensa Tanzania ndi kudzigulira malo mumpikisano wa 2018 World Cup.

Kuti ipitirire m’ndime ina ya mpikisanowu, timu ya Malawi ikuyenera kuchinya zigoli zosachepera ziwiri pambali polepheretsa alendo a kumpoto kwa dziko linowa kukoleka mpira muukonde.

Mtawali akuti mawa Flames idya monona
Mtawali akuti mawa Flames idya monona

Izi zili chonchi potsatira kugonja kwa Flames 2-0 pabwalo la Benjamin Mkapa ku Tanzania Lachitatu. Malawi itapambana 3-1 m’masewero achiwiri mawa, idzafanana zigoli ndi alendowa koma siidzakhalabe ndi mwayi wodumphira mu ndime ina ya mpikisanowu chifukwa malamulo amati zikatere, yemwe adapeza chigoli pabwalo la ena ndiwo akatswiri.

Koma mpira ukathera 2-0 mokomera Amalawi, tikhala kuti tafanana mphamvu ndipo pakayenera kulowa m’ndime ya kapherachoka wa mapenote kuti papezeke oyalula mphasa ndi kulowa m’ndime yachiwiri yodzakumana ndi timu ya dziko la Algeria.

“Nzotheka kupambana ndi zigoli zochuluka Lamulungu likudzali. Tinaluza ku Tanzania chifukwa chochinyitsa zigoli zopepera. Koma pano mavuto onse takonza ndipo tili okonzeka kuchotsa chitonzo chomwe tili nacho pakalipano,” adatero Mtawali m’sabatayi.

Komadi timumvere mphunzitsiyu zoti chilipo chipambano chokwanira mawa? Sitigwiritsidwanso fuwa la moto?

“Zitengera ndi mmene alowetsere osewera komanso momwe osewerawo adzadziperekere. Nkofunika tidzalimbikire kuthira nkhondo kutsogolo kwathu mowirikiza. Komanso tisadzawapatse adani mpata wobwerabwera kugolo lathu. Mwayi ulipo,” adatero kadaulo woona za masewero a mpira Charles Nyirenda.

Nyirenda, yemwe adakhalapo mkulu wa bungwe la masewero a mpira mdziko muno la FAM, adaonjezera kuti ochemerera mpira asadzafooke polimbikitsa osewera a dziko lino ndi mingoli yopereka chikhulupiliro.

Pamene Malawi imakomana ndi Tanzania Lachitatu, Mtawali adali atachotsa komanso kuonjezera osewera ena amene adapatsidwa mpata m’masewero okumana ndi Swaziland kwawo mumpikisano wa Africa Cup of Nations omwe adathera 2-2.

Iye adachotsa John Lanjesi kumbuyo ndi kuseweretsapo Miracle Gabeya ndipo adachotsanso Richard Chipuwa pagolo ndi kuikapo Simplex Nthala. Kutsogolo, adaikako Chawanangwa Kaonga mmalo mwa Chiukepo Msowoya yemwe adavulala.

Related Articles

Back to top button