Chichewa

Ntchito yasowa, wayamba ulimi wa kabichi

Listen to this article

 

Adabwera m’tauni ya Blantyre kudzasaka ntchito atamaliza Fomu 4. Adaponda paliponse kukasaka ntchito, makalata chilembelenicho ndi satifiketi yake ya Malawi School Certificate of Education (MSCE) koma palibe amene adamutenga. Yankho lidali lobwerera kumudzi kuti akangoyamba ulimi. Lero ulimi wa kabichi wayamba kumupatsa ndalama, wagula ng’ombe ziwiri, njinga, nkhuku komanso wamangitsa nyumba. Iyi ndiyo nkhani ya Patrick Khuliwa, yemwe akucheza ndi BOBBY KABANGO.

Kodi tingachezeko, wawa?

Kwambiri, palibe choletsa. Kaya mufuna ticheze nkhani zanji potitu tangokumana kumunda kuno.

 

Mbiri yanu komanso ulimi wa kabichi…

Vuto palibe, uwu ndi munda wanga, ndalima ndekha ndiye palibe pamene pangandivute kufotokoza.

Khuliwa akuti watola chikwama muulimi wa kabichi
Khuliwa akuti watola chikwama muulimi wa kabichi

Koma mbiri yanu ndi yotani?

Ndimachokera m’mudzi mwa Mulunguzi kwa T/A Juma m’boma la Mulanje. Ndili ndi satifiketi ya Fomu 4 yomwe ndidapeza mu 2007. Nditakhoza, ndidapita ku Blantyre monga ambiri amachitira komwe ndimakasaka maganyu. Achimwene, ndidavutika osati masewera, ntchito zikusowa. Zoti ndakhoza mayeso a Fomu 4 ngati bodza, ena ake amati mwina ndiyese ntchito za m’nyumba koma malipiro ake adali ochepa. Mapeto ake ndidabwerera n’kudzayamba ulimi wa kabichi.

Ulimiwu mudayamba liti?

Mu 2007 momwemo nditabwerako kutauni.

 

Chaka chino mwalima munda wokula bwanji? Nanga mukupeza zotani?

Ndalima theka la ekala. Munda umenewu chaka chino ndakolola matumba 20 a kabichi olemera makilogalamu 100 lililonse.

 

Mwapha ndalama zingati?

Thumba limodzi ndimagulitsa K9 000, pamatumba 20 ndidapeza K180 000 koma kabichi wina ndimagulitsira kumunda konkuno.

 

Msika mumaupeza bwanji?

Panopa palibenso nthawi yokayang’ana msika chifukwa mavenda akumadzagula kumunda konkuno koma chomwe tikuonetsetsa n’chakuti mtengo uzikhala wabwino. Monga poyamba timagulitsa K7 000 pa thumba limodzi koma pano lachita kukwera.

 

Pa chaka mukumalima kangati?

Nthawi ya mvula ndimalima kamodzi, koma mvula ikangotha ndimalima kabichi wamthirira yemwe ndikumalima kawiri, kusonyeza kuti ndikumalima katatu.

 

Uyu ali m’mundayu ndi wachingati?

Wachiwiri. Ndayambanso kukolola moti sabata ino ndikumaliza kukolola ndipo ndayamba kale kulima wina. Kutereku mbali inayo ndabzala kale. Pofika December ndikhala ndikukolola kusonyeza kuti ndidzakhala ndikukonzekera ulimi wa mvula.

 

Ulimi woyamba ndi wachiwiriwu mwapeza ndalama zingati?

Kupatula zochotsachotsa, ndalama yogwirika yomwe ndidaisunga idalipo K250 000. Ndalama zinazo ndimagwiritsira ntchito pakhomo.

 

Chiyambireni ulimiwu mwapangapo chiyani?

Ndamangitsa nyumba ya njerwa zootcha yomwenso ndi yamalata; ndagula ng’ombe ziwiri ndipo ndikulankhula pano zili m’khola mwake; komanso ndili ndi nkhuku ndi njinga. Ntchito zapakhomo zikuyenda kuchokera m’kabichi yemweyu.

 

Ganizo lopita m’tauni kukasaka ntchito lilipobe?

Hahaha! Amwene, ndingachite zimenezo? Akandipatsa ndalama zingati? Ineyo ndapeza mgodi ndipo nkhawa ndidapachika, palibe angandilembe ntchito koma ineyo kulemba munthu. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »